Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Zekariya 8:3 - Buku Lopatulika

3 Atero Yehova: Ndabwerera kudza ku Ziyoni, ndidzakhala pakati pa Yerusalemu; ndi Yerusalemu adzatchedwa, Mzinda wa choonadi; ndi phiri la Yehova wa makamu, Phiri lopatulika.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Atero Yehova: Ndabwerera kudza ku Ziyoni, ndidzakhala pakati pa Yerusalemu; ndi Yerusalemu adzatchedwa, Mudzi wa choonadi; ndi phiri la Yehova wa makamu, Phiri lopatulika.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Ine Chauta Wamphamvuzonse mau anga ndi aŵa: Tsopano ndidzabweranso ku phiri la Ziyoni, ndidzakhalanso ku Yerusalemu. Yerusalemuyo adzatchedwa Mzinda Wokhulupirika. Phiri la Ine Chauta Wamphamvuzonse lidzatchedwa Phiri Loyera.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Yehova akuti, “Ndidzabwerera ku Ziyoni ndi kukakhala ku Yerusalemu. Pamenepo Yerusalemu adzatchedwa Mzinda wa Choonadi ndipo phiri la Yehova Wamphamvuzonse lidzatchedwa Phiri Lopatulika.”

Onani mutuwo Koperani




Zekariya 8:3
39 Mawu Ofanana  

Koma Ine ndadzoza mfumu yanga Pa Ziyoni, phiri langa loyera.


Yehova ndiye wamkulu, ayenera kulemekezekadi, m'mzinda wa Mulungu wathu, m'phiri lake loyera.


Ndipo ndidzakhala pakati pa ana a Israele, ndi kukhala Mulungu wao.


Mzinda wokhulupirika wasanduka wadama! Wodzala chiweruzowo! Chilungamo chinakhalamo koma tsopano ambanda.


ndidzabweza oweruza ako monga poyamba, ndi aphungu ako monga pachiyambi; pambuyo pake udzatchedwa Mzinda wolungama, mzinda wokhulupirika.


Sizidzaipitsa, sizidzasakaza m'phiri langa lonse loyera, chifukwa kuti dziko lapansi lidzadzaza ndi odziwa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.


Tafuula, takuwa iwe, wokhala mu Ziyoni, chifukwa Woyera wa Israele wa m'kati mwako ali wamkulu.


Pamenepo chiweruzo chidzakhala m'chipululu, ndi chilungamo chidzakhala m'munda wobalitsa.


Ndipo ana aamuna a iwo amene anavuta iwe adzafika, nadzakugwadira; ndipo iwo onse amene anakuchepetsa iwe adzagwadira kumapazi ako, nadzakutcha iwe, Mzinda wa Yehova, Ziyoni wa Woyera wa Israele.


Mmbulu ndi mwanawankhosa zidzadyera pamodzi; ndi mkango udzadya udzu ngati ng'ombe; ndi fumbi lidzakhala chakudya cha njoka; sizidzapwetekana, kapena kusakazana m'phiri langa lonse lopatulika, ati Yehova.


Ndipo iwo adzatenga abale anu onse mwa amitundu onse akhale nsembe ya kwa Yehova; adzabwera nao pa akavalo, ndi m'magaleta, ndi m'machila, ndi pa nyuru, ndi pa ngamira, kudza kuphiri langa lopatulika ku Yerusalemu, ati Yehova, monga ana a Israele abwera nazo nsembe zao m'chotengera chokonzeka kunyumba ya Yehova.


Taonani, ine ndi ana amene Yehova wandipatsa ine, tili zizindikiro ndi zodabwitsa mwa Israele, kuchokera kwa Yehova wa makamu, amene akhala m'phiri la Ziyoni.


Bwanji mukhala ngati munthu wodabwa, ngati munthu wamphamvu wosatha kupulumutsa? Koma Inu, Yehova, muli pakati pathu, titchedwa ndi dzina lanu; musatisiye.


Mika Mmoreseti ananenera masiku a Hezekiya mfumu ya Yuda; ndipo iye ananena kwa anthu onse a Yuda, kuti, Yehova wa makamu atero: Ziyoni adzalimidwa ngati munda, Yerusalemu adzakhala miunda, ndi phiri la nyumba longa misanje ya nkhalango.


Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, Kawirinso adzanena mau awa m'dziko la Yuda ndi m'mizinda yake, pamene ndibwezanso undende wao; Yehova akudalitse iwe, wokhalamo chilungamo, iwe phiri lopatulika.


Masiku omwewo Yuda adzapulumutsidwa, ndi Yerusalemu adzakhala mokhulupirika; ili ndi dzina adzatchedwa nalo, Yehova ndiye chilungamo chathu.


Pozungulira pake ndipo mikono zikwi khumi mphambu zisanu ndi zitatu, ndi dzina la mzindawo kuyambira tsiku ilo lidzakhala, Yehova ali pomwepo.


Ambuye, monga mwa chilungamo chanu chonse, mkwiyo wanu ndi ukali wanu zitembenuketu, zichoke kumzinda wanu Yerusalemu, phiri lanu lopatulika; pakuti mwa zochimwa zathu, ndi mphulupulu za makolo athu, Yerusalemu ndi anthu anu asanduka chotonza cha onse otizungulira.


Momwemo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu wakukhala mu Ziyoni, phiri langa lopatulika; pamenepo Yerusalemu adzakhala wopatulika, osapitanso alendo pakati pake,


Ndipo ndidzayeretsa mwazi wao umene sindinauyeretsa, pakuti Yehova akhala mu Ziyoni.


Koma kudzachitika masiku otsiriza, kuti phiri la nyumba ya Yehova lidzakhazikika pamwamba pa mapiri, nilidzakuzika pamwamba pa zitunda; ndi mitundu ya anthu idzayendako.


Otsala a Israele sadzachita chosalungama, kapena kunena mabodza; ndi m'kamwa mwao simudzapezeka lilime lonyenga; pakuti adzadya nadzagona pansi, ndi palibe wakuwaopsa.


Chifukwa chake atero Yehova: Ndabwera kudza ku Yerusalemu ndi zachifundo; nyumba yanga idzamangidwamo, atero Yehova wa makamu, ndipo adzayesa Yerusalemu ndi chingwe.


Tsiku ilo ndidzaika akalonga a Yuda ngati phale la moto pansi pa nkhuni, ndi ngati muuni wamoto mwa mitolo ya tirigu; ndipo adzatha mitundu yonse ya anthu pozungulirapo, kudzanja lamanja ndi lamanzere; ndipo Yerusalemu adzakhalanso m'malo mwake, mu Yerusalemu.


Dziko lonse lidzasandulika, lidzanga chidikha, kuyambira ku Geba kufikira ku Rimoni, kumwera kwa Yerusalemu; ndipo pali uwupo padzakhala ponyamuka, ndipo udzakhala m'malo mwake, kuyambira ku Chipata cha Benjamini kufikira ku malo a chipata choyamba, kufikira ku Chipata cha Kungodya, ndi kuyambira Nsanja ya Hananele kufikira ku zoponderamo mphesa za mfumu.


Izi ndizo muzichite: Nenani choonadi yense ndi mnzake; weruzani zoona ndi chiweruzo cha mtendere m'zipata zanu;


Atero Yehova wa makamu: Kusala kwa mwezi wachinai, ndi kusala kwa mwezi wachisanu, ndi kusala kwa mwezi wachisanu ndi chiwiri, ndi kusala kwa mwezi wakhumi kukhale kwa nyumba ya Yuda chimwemwe ndi chikondwerero, ndi nyengo zoikika zosekerera; chifukwa chake kondani choonadi ndi mtendere.


Ndipo Mau anasandulika thupi, nakhazikika pakati pa ife, ndipo tinaona ulemerero wake, ulemerero wonga wa wobadwa yekha wa Atate, wodzala ndi chisomo ndi choonadi.


Yesu anayankha nati kwa iye, Ngati wina akonda Ine, adzasunga mau anga; ndipo Atate wanga adzamkonda, ndipo tidzadza kwa iye, ndipo tidzayesa kwa iye mokhalamo.


Ndipo chiphatikizo chake nchanji ndi Kachisi wa Mulungu ndi wa mafano? Pakuti ife ndife Kachisi wa Mulungu wamoyo; monga Mulungu anati, Ndidzakhalitsa mwa iwo, ndipo ndidzayendayenda mwa iwo; ndipo ndidzakhala Mulungu wao, ndi iwo adzakhala anthu anga.


pakuti mwa Iye chikhalira chidzalo cha Umulungu m'thupi,


Ndipo ananditenga mu Mzimu kunka kuphiri lalikulu ndi lalitali, nandionetsa mzinda wopatulikawo, Yerusalemu, wotsika mu Mwamba kuchokera kwa Mulungu,


ndipo simudzalowa konse momwemo kanthu kalikonse kosapatulidwa kapena iye wakuchita chonyansa ndi bodza; koma iwo okha olembedwa m'buku la moyo la Mwanawankhosa.


Ndipo ndinamva mau aakulu ochokera ku mpando wachifumu, ndi kunena Taonani, chihema cha Mulungu chili mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nao, ndi iwo adzakhala anthu ake, ndi Mulungu yekha adzakhala nao, Mulungu wao;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa