Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Zekariya 8:4 - Buku Lopatulika

4 Atero Yehova wa makamu: M'miseu ya Yerusalemu mudzakhalanso amuna ndi akazi okalamba, yense ndi ndodo yake m'dzanja lake chifukwa cha ukalamba wake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Atero Yehova wa makamu: M'miseu ya Yerusalemu mudzakhalanso amuna ndi akazi okalamba, yense ndi ndodo yake m'dzanja lake chifukwa cha ukalamba wake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 “Ine Chauta Wamphamvuzonse ndikunena kuti, amuna ndi akazi okalamba, oyenda ndi ndodo chifukwa cha ukalamba, adzayendanso m'miseu ya Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Abambo ndi amayi okalamba adzakhalanso mʼmisewu ya mu Yerusalemu, aliyense ali ndi ndodo mʼmanja mwake chifukwa cha kuchuluka kwa masiku ake.

Onani mutuwo Koperani




Zekariya 8:4
12 Mawu Ofanana  

Namwalira Yobu, wokalamba ndi wa masiku ochuluka.


Udzafika kumanda utakalamba, monga abwera nao mtolo wa tirigu m'nyengo yake.


akaukanso, nakayendayenda pabwalo ndi ndodo yake, womkanthayo azikhala womasuka; pakutsotsa pake pokha azimbwezera, namchizitse konse.


Ndipo namwali adzasangalala m'masewero, ndi anyamata ndi nkhalamba pamodzi; pakuti ndidzasandutsa kulira kwao kukhale kukondwera, ndipo ndidzatonthoza mitima yao, ndi kuwasangalatsa iwo asiye chisoni chao.


Ndipo Yuda ndi mizinda yake yonse adzakhalamo pamodzi; alimi, ndi okusa zoweta.


nanena naye, Thamanga, lankhula ndi mnyamata uyu, ndi kuti, Mu Yerusalemu mudzakhala anthu ngati m'midzi yopanda malinga, chifukwa cha kuchuluka anthu ndi zoweta momwemo.


Komatu mwayandikira kuphiri la Ziyoni, ndi mzinda wa Mulungu wamoyo, Yerusalemu wa Kumwamba, ndi kwa unyinji wochuluka wa angelo,


Ona, masiku alinkudza amene ndidzadula dzanja lako, ndi dzanja la nyumba ya kholo lako, kuti m'banja lako musakhalenso nkhalamba.


Ndipo udzaona masautso a mokhalamo Mulungu, m'malo mwa zabwino zonse Iye akadachitira Israele. Banja lako lidzakhala opanda nkhalamba chikhalire.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa