Ndipo Yowabu ananena ndi womuuzayo, Ndipo taona, unamuona, tsono unalekeranji kumkantha agwe pansi pomwepo? Ndipo ine ndikadakupatsa ndalama khumi ndi lamba.
Masalimo 143:3 - Buku Lopatulika Pakuti mdani alondola moyo wanga; apondereza pansi moyo wanga; andikhalitsa mumdima monga iwo adafa kale lomwe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti mdani alondola moyo wanga; apondereza pansi moyo wanga; andikhalitsa mumdima monga iwo adafa kale lomwe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mdani wandilondola, wavimviniza moyo wanga m'dothi, wandikhazika mu mdima, ngati anthu amene adafa kale. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mdani akundithamangitsa, iye wandipondereza pansi; wachititsa kuti ndikhale mu mdima ngati munthu amene anafa kale. |
Ndipo Yowabu ananena ndi womuuzayo, Ndipo taona, unamuona, tsono unalekeranji kumkantha agwe pansi pomwepo? Ndipo ine ndikadakupatsa ndalama khumi ndi lamba.
Ndipo Abinere anabwereza kunena kwa Asahele, Patuka pakunditsata ine. Ndidzakukanthiranji kukugwetsa pansi? Ndikatero ndidzaweramutsanso bwanji nkhope yanga kwa mbale wako Yowabu?
Tamverani kufuula kwanga; popeza ndisauka kwambiri; ndilanditseni kwa iwo akundilondola; popeza andipambana.
Athe nzeru nachite manyazi iwo akufuna moyo wanga; abwezedwe m'mbuyo nasokonezeke iwo akundipangira chiwembu.
Pakuti alendo andiukira, ndipo oopsa afunafuna moyo wanga; sadziikira Mulungu pamaso pao.
mdani alondole moyo wanga, naupeze; naupondereze pansi moyo wanga, naukhalitse ulemu wanga m'fumbi.
Ukani Yehova mu mkwiyo wanu, nyamukani chifukwa cha ukali wa akundisautsa; ndipo mugalamukire ine; mwalamulira chiweruzo.
Pamenepo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, Mafupa awa ndiwo nyumba yonse ya Israele; taonani, akuti, Mafupa athu auma, chiyembekezo chathu chatayika, talikhidwa.
Usandiseka, mdani wangawe; pakugwa ine ndidzaukanso; pokhala ine mumdima Yehova adzakhala kuunika kwanga.