Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 18:11 - Buku Lopatulika

11 Ndipo Yowabu ananena ndi womuuzayo, Ndipo taona, unamuona, tsono unalekeranji kumkantha agwe pansi pomwepo? Ndipo ine ndikadakupatsa ndalama khumi ndi lamba.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Ndipo Yowabu ananena ndi womuuzayo, Ndipo taona, unamuona, tsono unalekeranji kumkantha agwe pansi pomwepo? Ndipo ine ndikadakupatsa ndalama khumi ndi lamba.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Yowabu adafunsa munthuyo kuti, “Nanga bwanji sudamphere pomwepo? Ndikadakondwa ndipo ndikadakupatsa ndalama zasiliva khumi ndiponso lamba.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Yowabu anati kwa munthu amene anamuwuza zimenezi, “Ukuti chiyani! Unamuona? Nʼchifukwa chiyani sunamukanthire pansi pomwepo? Ndipo ine ndikanakupatsa ndalama za siliva khumi ndi lamba wausilikali.”

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 18:11
5 Mawu Ofanana  

Ndipo munthu wina anamuona, nauza Yowabu, nati, Onani, ndaona Abisalomu ali lende pathundu.


Munthuyo nanena ndi Yowabu, Ndingakhale ndikalandira ndalama chikwi m'dzanja langa, koma sindikadasamula dzanja langa pa mwana wa mfumu; pakuti m'kumva kwathu mfumu inalamulira inu ndi Abisai ndi Itai, kuti, Chenjerani munthu yense asakhudze mnyamatayo Abisalomu.


Ndipo munene ndi Amasa, Suli fupa langa ndi mnofu wanga kodi? Mulungu andilange naonjezepo ngati sudzakhala chikhalire kazembe wa khamu la ankhondo pamaso panga, m'malo mwa Yowabu.


Pakuti mdani alondola moyo wanga; apondereza pansi moyo wanga; andikhalitsa mumdima monga iwo adafa kale lomwe.


Mayendedwe a yense wopindula chuma monyenga ngotere; chilanda moyo wa eni ake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa