Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 18:12 - Buku Lopatulika

12 Munthuyo nanena ndi Yowabu, Ndingakhale ndikalandira ndalama chikwi m'dzanja langa, koma sindikadasamula dzanja langa pa mwana wa mfumu; pakuti m'kumva kwathu mfumu inalamulira inu ndi Abisai ndi Itai, kuti, Chenjerani munthu yense asakhudze mnyamatayo Abisalomu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Munthuyo nanena ndi Yowabu, Ndingakhale ndikalandira ndalama chikwi m'dzanja langa, koma sindikadasamula dzanja langa pa mwana wa mfumu; pakuti m'kumva kwathu mfumu inalamulira inu ndi Abisai ndi Itai, kuti, Chenjerani munthu yense asakhudze mnyamatayo Abisalomu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Koma munthuyo adauza Yowabu kuti, “Ngakhale ndikadalandira m'manja mwangamu ndalama zasiliva zokwanira 1,000, sindikadasamula dzanja langa kuti ndiphe mwana wa mfumu. Paja mfumu idakulamulani inu ndi Abisai ndi Itai, ife tilikumva, kuti, ‘Mumtchinjirize mwanayo Abisalomu chifukwa cha ine.’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Koma munthuyo anayankha kuti, “Ngakhale atandipatsa mʼmanja mwanga ndalama zasiliva 1,000, sindingatambasule dzanja langa kupha mwana wa mfumu. Ife tikumva, mfumu inalamula inu Abisai ndiponso Itai kuti, ‘Mutetezeni mnyamatayo Abisalomu chifukwa cha ine!’

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 18:12
3 Mawu Ofanana  

Ndipo Yowabu ananena ndi womuuzayo, Ndipo taona, unamuona, tsono unalekeranji kumkantha agwe pansi pomwepo? Ndipo ine ndikadakupatsa ndalama khumi ndi lamba.


Ndipo mfumu inalamulira Yowabu ndi Abisai ndi Itai, kuti, Chifukwa cha ine muchite mofatsa ndi mnyamatayo, Abisalomu. Ndipo anthu onse anamva pamene mfumu inalamulira atsogoleriwo za Abisalomu.


Ndipo anauza Yowabu, Onani mfumu ilikulira misozi, nilira Abisalomu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa