Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mika 7:8 - Buku Lopatulika

8 Usandiseka, mdani wangawe; pakugwa ine ndidzaukanso; pokhala ine mumdima Yehova adzakhala kuunika kwanga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Usandiseka, mdani wangawe; pakugwa ine ndidzaukanso; pokhala ine mumdima Yehova adzakhala kuunika kwanga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Inu adani athu musatiseke. Tidagwa inde, koma tidzadzukanso. Ngakhale tikhale mu mdima, Chauta ndiye nyale yathu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Iwe mdani wanga, usandiseke! Ngakhale ndagwa, ndidzauka. Ngakhale ndikukhala mu mdima, Yehova ndiye kuwunika kwanga.

Onani mutuwo Koperani




Mika 7:8
46 Mawu Ofanana  

Ngati ndakondwera nalo tsoka la wondida, kapena kudzitukula pompeza choipa;


Kuunika kutulukira oongoka mtima mumdima; Iye ndiye wachisomo, ndi wansoni ndi wolungama.


Pakuti mdani alondola moyo wanga; apondereza pansi moyo wanga; andikhalitsa mumdima monga iwo adafa kale lomwe.


Iwowa anagonjeka, nagwa; koma ife tauka, ndipo takhala chilili.


Yehova ndiye kuunika kwanga ndi chipulumutso changa; ndidzaopa yani? Yehova ndiye mphamvu ya moyo wanga; ndidzachita mantha ndi yani?


Adani anga asandikondwerere ine monyenga; okwiya nane kopanda chifukwa asanditsinzinire.


Woipa akongola, wosabweza, koma wolungama achitira chifundo, napereka.


Angakhale akagwa, satayikiratu, pakuti Yehova agwira dzanja lake.


Pakuti ndinati, Asakondwerere ine; pakuterereka phazi langa, asadzikuze pa ine.


Pakuti Yehova Mulungu ndiye dzuwa ndi chikopa; Yehova adzapatsa chifundo ndi ulemerero; sadzakaniza chokoma iwo akuyenda angwiro.


Kuunika kufesekera wolungama, ndi chikondwerero oongoka mtima.


Inu a nyumba ya Yakobo, tiyeni, tiyende m'kuwala kwa Yehova.


ndi kunena kwa iwo amene ali omangidwa, Mukani, kwa iwo amene ali mumdima, Dzionetseni nokha. Iwo adzadya m'njira, ndi m'zitunda zonse zoti see mudzakhala busa lao.


Ndani ali mwa inu amene amaopa Yehova, amene amamvera mau a mtumiki wake? Iye amene ayenda mumdima, ndipo alibe kuunika, akhulupirire dzina la Yehova, ndi kutsamira Mulungu wake.


Anthu amene anayenda mumdima, aona kuwala kwakukulu; iwo amene anakhala m'dziko la mthunzi wa imfa, kuwala kwatulukira kwa iwo.


Kodi sunaseke Israele? Kodi iye anapezedwa mwa mbala? Pakuti nthawi zonse unena za iye, upukusa mutu.


Chifukwa mukondwa, chifukwa musekerera, inu amene mulanda cholowa changa, chifukwa muli onenepa monga ng'ombe yaikazi yoponda tirigu, ndi kulira ngati akavalo olimba;


Ndiponso udzati kwa iwo, Atero Yehova, Kodi adzagwa, osaukanso? Kodi wina adzachoka, osabweranso?


Pakuti atero Ambuye Yehova, Waomba manja, ndi kuvina, ndi kukondwera ndi chipeputso chonse cha moyo wako, kupeputsa dziko la Israele,


Monga momwe unakondwerera cholowa cha nyumba ya Israele, popeza chidapasuka, momwemo ndidzakuchitira iwe; udzakhala wopasuka, phiri la Seiri iwe, ndi Edomu lonse lonseli; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.


chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Zoonadi pa nsanje yanga yodya nayo moto ndinanena motsutsana nao amitundu otsala, ndi Edomu yense, amene anadzipatsira dziko langa likhale cholowa chao ndi chimwemwe cha mtima wonse, ndi mtima wopeputsa, kuti alande zake zonse zikhale zofunkha.


Tsiku lomwelo ndidzautsa msasa wa Davide udagwawo, ndi kukonzanso zopasuka zake; ndipo ndidzautsa zogumuka zake, ndi kuumanga monga masiku a kalelo;


Koma usapenyerera tsiku la mphwako, tsiku loyesedwa mlendo iye, nusasekerere ana a Yuda tsiku la kuonongeka kwao, kapena kuseka chikhakha tsiku lakupsinjika.


Imva zowawa, nuyesetse kubala, mwana wamkazi wa Ziyoni, ngati mkazi wakubala; pakuti udzatuluka m'mzinda tsopano, nudzakhala kuthengo, nudzafika ku Babiloni; komweko udzapulumutsidwa; komweko Yehova adzakuombola m'manja a adani ako.


Pamenepo mdani wanga adzachiona, ndi manyazi adzamkuta iye amene adati kwa ine, Ali kuti Yehova Mulungu wako? Maso anga adzamuona; tsopano adzampondereza ngati thope la m'miseu.


Tsiku ilo Yehova adzatchinjiriza okhala mu Yerusalemu; ndi iye wokhumudwa pakati pao tsiku lomwelo adzakhala ngati Davide; ndi nyumba ya Davide idzakhala ngati Mulungu, ngati mthenga wa Yehova pakati pao.


Koma inu akuopa dzina langa, dzuwa la chilungamo lidzakutulukirani, muli kuchiritsa m'mapiko mwake; ndipo mudzatuluka ndi kutumphatumpha ngati anaang'ombe onenepa otuluka m'khola.


anthu akukhala mumdima adaona kuwala kwakukulu, ndi kwa iwo okhala m'malo a mthunzi wa imfa, kuwala kunatulukira iwo.


Indetu, indetu, ndinena ndi inu, kuti mudzalira ndi kubuma maliro inu, koma dziko lapansi lidzakondwera; mudzachita chisoni inu, koma chisoni chanu chidzasandulika chimwemwe.


Pamenepo Yesu analankhulanso nao, nanena, Ine ndine kuunika kwa dziko lapansi; iye wonditsata Ine sadzayenda mumdima, koma adzakhala nako kuunika kwa moyo.


kukawatsegulira maso ao, kuti atembenuke kuchokera kumdima, kulinga kukuunika, ndi kuchokera ulamuliro wa Satana kulinga kwa Mulungu, kuti alandire iwo chikhululukiro cha machimo, ndi cholowa mwa iwo akuyeretsedwa ndi chikhulupiriro cha mwa Ine.


Pakuti Mulungu amene anati, Kuunika kudzawala kutuluka mumdima, ndiye amene anawala m'mitima yathu kutipatsa chiwalitsiro cha chidziwitso cha ulemerero wa Mulungu pankhope pa Yesu Khristu.


olondoleka, koma osatayika; ogwetsedwa, koma osaonongeka;


Ndipo pamzinda sipafunika dzuwa, kapena mwezi wakuuwalira; pakuti ulemerero wa Mulungu uunikira umenewu, ndipo nyali yake ndiye Mwanawankhosa.


Ndipo sikudzakhalanso usiku; ndipo sasowa kuunika kwa nyali, ndi kuunika kwa dzuwa; chifukwa Ambuye Mulungu adzawaunikira; ndipo adzachita ufumu kunthawi za nthawi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa