Mika 7:9 - Buku Lopatulika9 Ndidzasenza mkwiyo wa Yehova, chifukwa ndamchimwira, mpaka andinenera mlandu wanga, ndi kundiweruzira mlandu wanga; adzanditulutsira kwa kuunika, ndipo ndidzapenya chilungamo chake. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20149 Ndidzasenza mkwiyo wa Yehova, chifukwa ndamchimwira, mpaka andinenera mlandu wanga, ndi kundiweruzira mlandu wanga; adzanditulutsira kwa kuunika, ndipo ndidzapenya chilungamo chake. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa9 Tachimwira Chauta, nchifukwa chake tiyenera kupirira mkwiyo wake, mpaka atazenga mlandu wathu ndi kuugamula. Koma pambuyo pake adzatiloŵetsa m'kuŵala, ndipo tidzaona chipulumutso chake. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero9 Ndidzapirira mkwiyo wa Yehova, chifukwa ndinamuchimwira, mpaka ataweruza mlandu wanga ndi kukhazikitsa chilungamo changa. Iye adzanditulutsa ndi kundilowetsa mʼkuwunika; ndidzaona chilungamo chake. Onani mutuwo |
Ndipo pamene Davide anamva kuti Nabala adamwalira, iye anati, Alemekezedwe Yehova, amene anaweruza mlandu wa mtonzo wanga wochokera ku dzanja la Nabala, naletsa mnyamata wake pa choipa; ndipo Yehova anabwezera pamutu pa Nabala choipa chake. Ndipo Davide anatumiza wokamfunsira Abigaile, zakuti amtengere akhale mkazi wake.