Ndipo tsopano, kamphindi, Yehova Mulungu wathu wationetsa chisomo, kutisiyira chipulumutso, ndi kutipatsa chichiri m'malo mwake mopatulika; kuti Mulungu wathu atipenyetse m'maso mwathu, ndi kutitsitsimutsa pang'ono mu ukapolo wathu.
Masalimo 13:3 - Buku Lopatulika Penyani, ndiyankheni, Yehova Mulungu wanga. Penyetsani maso anga, kuti ndingagone tulo ta imfa; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Penyani, ndiyankheni, Yehova Mulungu wanga. Penyetsani maso anga, kuti ndingagone tulo ta imfa; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mundikumbukire ndipo mundiyankhe, Inu Chauta, Mulungu wanga. Mundiwunikire kuti ndingagone tulo tofa nato. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndiyangʼaneni ndi kundiyankha, Inu Yehova Mulungu wanga. Walitsani maso anga kuti ndingafe; |
Ndipo tsopano, kamphindi, Yehova Mulungu wathu wationetsa chisomo, kutisiyira chipulumutso, ndi kutipatsa chichiri m'malo mwake mopatulika; kuti Mulungu wathu atipenyetse m'maso mwathu, ndi kutitsitsimutsa pang'ono mu ukapolo wathu.
Ndidzakondwera ndi kusangalala m'chifundo chanu, pakuti mudapenya zunzo langa; ndipo mudadziwa mzimu wanga mu nsautso yanga.
Ndichitireni chifundo, Yehova; penyani kuzunzika kwanga kumene andichitira ondidawo, inu wondinyamula kundichotsa kuzipata za imfa.
Pamene atentha, ndidzakonza madyerero ao, ndidzawaledzeretsa, kuti asangalale, agone chigonere, asanyamuke, ati Yehova.
Ndipo ndidzaledzeretsa akulu ake ndi anzeru ake, akazembe ake ndi ziwanga zake, ndi anthu ake olimba; ndipo adzagona chigonere, sadzanyamuka, ati Mfumu, dzina lake ndi Yehova wa makamu.
kuunika kukhale chivumbulutso cha kwa anthu a mitundu, ndi ulemerero wa anthu anu Israele.
Ndipo pamzinda sipafunika dzuwa, kapena mwezi wakuuwalira; pakuti ulemerero wa Mulungu uunikira umenewu, ndipo nyali yake ndiye Mwanawankhosa.
Koma Yonatani sanamve m'mene atate wake analumbirira anthu; chifukwa chake iye anatambalitsa ndodo ya m'dzanja lake, naitosa m'chisa cha uchi, naika dzanja lake pakamwa pake; ndipo m'maso mwake munayera.
Ndipo Yonatani anati, Atate wanga wavuta dziko; onani m'maso mwanga mwayera, chifukwa ndinalawako pang'ono uchiwu.