1 Samueli 14:27 - Buku Lopatulika27 Koma Yonatani sanamve m'mene atate wake analumbirira anthu; chifukwa chake iye anatambalitsa ndodo ya m'dzanja lake, naitosa m'chisa cha uchi, naika dzanja lake pakamwa pake; ndipo m'maso mwake munayera. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201427 Koma Yonatani sanamve m'mene atate wake analumbirira anthu; chifukwa chake iye anatambalitsa ndodo ya m'dzanja lake, naitosa m'chisa cha uchi, naika dzanja lake pakamwa pake; ndipo m'maso mwake munayera. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa27 Koma Yonatani anali asanamve za temberero la bambo wake lija. Choncho adatosa chisa cha njuchi ndi nsonga ya ndodo imene inali m'manja mwake, naika uchi wake pakamwa naadya. Atatero m'maso mwake mudachita kuti ngwee. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero27 Koma Yonatani sanamve kuti abambo ake anawalumbirira anthu aja choncho anatenga ndodo yake imene inali mʼdzanja lake ndipo anayipisa mu chisa cha njuchi. Choncho iye anadya uchiwo ndipo mʼmaso mwake munayera. Onani mutuwo |