Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 18:28 - Buku Lopatulika

28 Pakuti Inu muyatsa nyali yanga; Yehova, Mulungu wanga, aunikira mdima wanga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

28 Pakuti Inu muyatsa nyali yanga; Yehova, Mulungu wanga, aunikira mdima wanga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

28 Ndithu, Inu mumayatsa nyale ya moyo wanga. Chauta, Mulungu wanga, amandiwunikira mu mdima.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

28 Inu Yehova, sungani nyale yanga kuti iziyakabe; Mulungu wanga wasandutsa mdima wanga kukhala kuwunika.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 18:28
15 Mawu Ofanana  

Pakuti Inu ndinu nyali yanga, Yehova; ndipo Yehova adzaunika mumdima mwanga.


Ndipo ndidzamninkha mwana wake fuko limodzi, kuti Davide mtumiki wanga akhale chikhalire ndi nyali pamaso panga mu Yerusalemu, mzinda umene ndinadzisankhira kuikapo dzina langa.


Koma chifukwa cha Davideyo Yehova Mulungu wake anampatsa nyali mu Yerusalemu, kumuikira mwana wake pambuyo pake, ndi kukhazikitsa Yerusalemu;


Kuunikaku kudzada m'hema mwake, ndi nyali yake ya pamwamba pake idzazima.


muja nyali yake inawala pamutu panga, ndipo ndi kuunika kwake ndinayenda mumdima;


Kuunika kutulukira oongoka mtima mumdima; Iye ndiye wachisomo, ndi wansoni ndi wolungama.


Apo ndidzaphukitsira Davide nyanga; ndakonzeratu wodzozedwa wanga nyali.


Mzimu wa munthu ndiwo nyali ya Yehova; usanthula m'kati monse mwa mimba.


Maso a munthu akuyang'anira kumwamba adzatsitsidwa, ndi kudzikweza kwa anthu kudzaweramitsidwa pansi; ndipo Yehova yekha adzakwezedwa tsiku limenelo.


Chifukwa padzakhala tsiku la Yehova wa makamu pa zonse zonyada ndi zakudzikuza, ndi pa zonse zotukulidwa; ndipo zidzatsitsidwa;


Ndipo ndidzayendetsa akhungu m'khwalala, limene iwo salidziwa, m'njira zimene iwo sazidziwa ndidzawatsogolera; ndidzawalitsa mdima m'tsogolo mwao, ndi kulungamitsa malo okhota. Zinthu izi Ine ndidzachita, ndipo sindidzawasiya.


Chifukwa cha Ziyoni sindidzakhala chete, ndi chifukwa cha Yerusalemu sindidzapuma, kufikira chilungamo chake chidzatuluka monga kuyera, ndi chipulumutso chake monga nyali yoyaka.


anthu akukhala mumdima adaona kuwala kwakukulu, ndi kwa iwo okhala m'malo a mthunzi wa imfa, kuwala kunatulukira iwo.


Kuwalitsira iwo okhala mumdima ndi mthunzi wa imfa; kulunjikitsa mapazi athu mu njira ya mtendere.


Koma inu ndinu mbadwa yosankhika, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu a mwini wake, kotero kuti mukalalikire zoposazo za Iye amene anakuitanani mutuluke mumdima, mulowe kuunika kwake kodabwitsa;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa