Akapanda kumanga nyumba Yehova, akuimanga agwiritsa ntchito chabe; akapanda kusunga mzinda Yehova, mlonda adikira chabe.
Masalimo 121:3 - Buku Lopatulika Sadzalola phazi lako literereke: Iye amene akusunga sadzaodzera. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Sadzalola phazi lako literereke: Iye amene akusunga sadzaodzera. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Sadzalola phazi lako kuti literereke, Iye amene amakusunga sadzaodzera. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Sadzalola kuti phazi lako literereke; Iye amene amakusunga sadzawodzera. |
Akapanda kumanga nyumba Yehova, akuimanga agwiritsa ntchito chabe; akapanda kusunga mzinda Yehova, mlonda adikira chabe.
Yehova adzamsunga, nadzamsunga ndi moyo, ndipo adzadalitsika padziko lapansi, ndipo musampereke ku chifuniro cha adani ake.
Koma Inu, Mulungu, mudzawatsitsira kudzenje la chionongeko. Anthu okhetsa mwazi ndi achinyengo masiku ao sadzafikira nusu; koma ine ndidzakhulupirira Inu.
Ine Yehova ndiusunga uwo; ndidzauthirira madzi nthawi zonse; ndidzausunga usiku ndi usana, kuti angauipse.
amene musungidwa ndi mphamvu ya Mulungu mwa chikhulupiriro, kufikira chipulumutso chokonzeka kukavumbulutsidwa nthawi yotsiriza.
Adzasunga mapazi a okondedwa ake, koma oipawo adzawakhalitsa chete mumdima; pakuti palibe munthu adzapambana ndi mphamvu.