Masalimo 102:8 - Buku Lopatulika Adani anga anditonza tsiku lonse; akundiyalukirawo alumbirira ine. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Adani anga anditonza tsiku lonse; akundiyalukirawo alumbirira ine. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsiku lonse adani anga amandichita chipongwe, onse ondinyoza amatchula dzina langa potemberera. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsiku lonse adani anga amandichita chipongwe; iwo amene amandinyoza, amagwiritsa ntchito dzina langa ngati temberero. |
chifukwa cha mau a mdani, chifukwa cha kundipsinja woipa; pakuti andisenza zopanda pake, ndipo adana nane mumkwiyo.
Chotonza chandiswera mtima, ndipo ndidwala ine; ndipo ndinayembekeza wina wondichitira chifundo, koma palibe; ndinayembekeza onditonthoza mtima, osawapeza.
Chimene adani anu, Yehova, atonza nacho; chimene atonzera nacho mayendedwe a wodzozedwa wanu.
Ndipo mudzasiya dzina lanu likhale chitemberero kwa osankhidwa anga, ndipo Ambuye Yehova adzakupha iwe, nadzatcha atumiki ake dzina lina;
ndipo am'nsinga onse a Yuda amene ali mu Babiloni adzatemberera pali iwo, kuti, Yehova akuchitire iwe monga Zedekiya ndi Ahabu, amene mfumu ya ku Babiloni inaotcha m'moto;
Ndipo ndinawalanga kawirikawiri m'masunagoge onse, ndi kuwakakamiza anene zamwano; ndipo pakupsa mtima kwakukulu pa iwo ndinawalondalonda ndi kuwatsata ngakhale kufikira kumizinda yakunja.
Pakuti Khristunso sanadzikondweretse yekha; koma monga kwalembedwa, Minyozo ya iwo amene anakunyoza iwe inagwa pa Ine.