Masalimo 101:4 - Buku Lopatulika Mtima wopulukira udzandichokera; sindidzadziwana naye woipa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mtima wopulukira udzandichokera; sindidzadziwana naye woipa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndidzakhala kutali ndi anthu a mtima woipa, sindidzalola choipa chilichonse kuloŵa mwa ine. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anthu a mtima wokhota adzakhala kutali ndi ine; ine sindidzalola choyipa chilichonse kulowa mwa ine. |
Chokani kwa ine, nonsenu akuchita zopanda pake; pakuti wamva Yehova mau a kulira kwanga.
Kuopa Yehova ndiko kuda zoipa; kunyada, ndi kudzikuza, ndi njira yoipa, ndi m'kamwa mokhota, ndizida.
Ndipo pamenepo ndidzafukulira iwo, Sindinakudziweni inu nthawi zonse; chokani kwa Ine, inu akuchita kusaweruzika.
Koma ndithu maziko a Mulungu aimika pokhazikika, ndi kukhala nacho chizindikiro ichi, Ambuye azindikira iwo amene ali ake; ndipo, Adzipatule kwa chosalungama yense wakutchula dzina la Ambuye.