Genesis 7:5 - Buku Lopatulika Ndipo anachita Nowa monga mwa zonse anamlamulira iye Yehova. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anachita Nowa monga mwa zonse anamlamulira iye Yehova. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo Nowa adachita zonse zimene Mulungu adamlamula. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Nowa anachita zonse zimene Yehova anamulamulira. |
Zimene zinalowazo, zinalowa yamphongo ndi yaikazi zamoyo zonse, monga momwe Mulungu anamlamulira iye: ndipo Yehova anamtsekera iye.
Potero anatsiriza ntchito yonse ya Kachisi wa chihema chokomanako; ndipo ana a Israele adachita monga mwa zonse Yehova adamuuza Mose, anachita momwemo.
Koma Yesu anayankha, nati kwa iye, Balola tsopano: pakuti kuyenera ife kukwaniritsa chilungamo chonse motero. Pamenepo anamlola Iye.
Koma Iye anayankha, nati kwa iwo, Amai wanga ndi abale anga ndiwo amene akumva mau a Mulungu, nawachita.
ndipo popezedwa m'maonekedwe ngati munthu, anadzichepetsa yekha, nakhala womvera kufikira imfa, ndiyo imfa ya pamtanda.