Genesis 6:5 - Buku Lopatulika Ndipo anaona Yehova kuti kuipa kwa anthu kunali kwakukulu padziko lapansi, ndiponso kuti ndingaliro zonse za maganizo a mitima yao zinali zoipabe zokhazokha. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anaona Yehova kuti kuipa kwa anthu kunali kwakukulu pa dziko lapansi, ndiponso kuti ndingaliro zonse za maganizo a mitima yao zinali zoipabe zokhazokha. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamene Chauta adaona kuti anthu a pa dziko lapansi aipa koopsa, ndiponso kuti mitima yao inali yodzaza ndi maganizo oipa, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamene Yehova anaona kuti kuyipa kwa munthu pa dziko lapansi kunali kwakukulu ndi kuti nthawi zonse amalingalira ndi kukhumbira kuchita zoyipa zokhazokha, |
Ndipo Yehova anamva chonunkhira chakukondweretsa; nati Yehova m'mtima mwake, Sindidzatembereranso konse nthaka chifukwa cha munthu; pakuti ndingaliro ya mtima wa munthu ili yoipa kuyambira pa unyamata wake; sindidzaphanso konse zinthu zonse zamoyo, monga momwe ndachitiramo.
Mulungu m'mwamba anaweramira pa ana a anthu, kuti aone ngati aliko wanzeru, wakufuna Mulungu.
Taonani, ichi chokha ndachipeza kuti Mulungu analenga anthu oongoka mtima; koma iwowo afunafuna malongosoledwe a mitundumitundu.
Ichi ndi choipa m'zonse zichitidwa pansi pano, chakuti kanthu kamodzi kagwera onse; indetu, mtimanso wa ana a anthu wadzala udyo, ndipo misala ili m'mtima wao akali ndi moyo, ndi pamenepo apita kwa akufa.
Iwe Yerusalemu, utsuke mtima wako kuchotsa zoipa kuti upulumuke. Maganizo ako achabe agona mwako masiku angati?
Pamenepo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, wapenya kodi chochita akulu a nyumba ya Israele mumdima, aliyense m'chipinda chake cha zifanizo? Pakuti ati, Yehova satipenya, Yehova wataya dziko.
Pakuti mumtima muchokera maganizo oipa, zakupha, zachigololo, zachiwerewere, zakuba, za umboni wonama, zamwano;
Ndipo kungakhale, akamva mau a lumbiro ili adzadzidalitsa m'mtima mwake, ndi kuti, Ndidzakhala nao mtendere, ndingakhale ndiyenda nao mtima wanga wopulukira, kuledzera nditamva ludzu;
Pakuti kale ifenso tinali opusa, osamvera, onyengeka, akuchitira ukapolo zilakolako ndi zokondweretsa za mitundumitundu, okhala m'dumbo ndi njiru, odanidwa, odana wina ndi mnzake.
imene inakhala yosamvera kale, pamene kuleza mtima kwa Mulungu kunalindira, m'masiku a Nowa, pokhala m'kukonzeka chingalawa, m'menemo owerengeka, ndiwo amoyo asanu ndi atatu, anapulumutsidwa mwa madzi;