Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Mlaliki 7:29 - Buku Lopatulika

29 Taonani, ichi chokha ndachipeza kuti Mulungu analenga anthu oongoka mtima; koma iwowo afunafuna malongosoledwe a mitundumitundu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

29 Taonani, ichi chokha ndachipeza kuti Mulungu analenga anthu oongoka mtima; koma iwowo afunafuna malongosoledwe a mitundumitundu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

29 Ndidapeza chokhachi chakuti Mulungu pomulenga munthu, adampatsa mtima wolungama, koma anthu amatsata njira zaozao zambirimbiri.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

29 Chokhacho chimene ndinachipeza ndi ichi: Mulungu analenga munthu, anamupatsa mtima wolungama, koma anthu anatsatira njira zawozawo zambirimbiri.”

Onani mutuwo Koperani




Mlaliki 7:29
20 Mawu Ofanana  

Ili ndi buku la mibadwo ya Adamu. Tsiku lomwe Mulungu analenga munthu anamlenga m'chifanizo cha Mulungu;


Ndipo anamkwiyitsa nazo zochita zao; kotero kuti mliri unawagwera.


Ndipo anadziipsa nazo ntchito zao, nachita chigololo nao machitidwe ao.


Munawayankha, Yehova Mulungu wathu: munawakhalira Mulungu wakuwakhululukira, mungakhale munabwezera chilango pa zochita zao.


Ndani akunga wanzeru? Ndani adziwa tanthauzo la mau? Nzeru ya munthu iwalitsa nkhope yake, kuduwa kwa nkhope yake ndi kusanduka.


Pakuti anthu anga apusa, sandidziwa Ine; ali ana opulukira sazindikira; ali ochenjera kuchita choipa koma kuchita chabwino sakudziwa.


Unali wangwiro m'njira zako chilengedwere iwe, mpaka chinapezeka mwa iwe chosalungama.


Pakuti kale ifenso tinali opusa, osamvera, onyengeka, akuchitira ukapolo zilakolako ndi zokondweretsa za mitundumitundu, okhala m'dumbo ndi njiru, odanidwa, odana wina ndi mnzake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa