Ndipo Abramu anatenga Sarai mkazi wake, ndi Loti mwana wa mphwake, ndi chuma chao chimene anasonkhanitsa, ndi miyoyo imene anabala mu Harani; natuluka kunka ku dziko la Kanani, ndipo anadza ku dziko la Kanani.
Genesis 48:21 - Buku Lopatulika Ndipo Israele anati kwa Yosefe, Taona, ndilinkufa ine; Mulungu adzakhala ndi iwe, adzakubwezanso iwe ku dziko la makolo ako. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Israele anati kwa Yosefe, Taona, ndilinkufa ine; Mulungu adzakhala ndi iwe, adzakubwezanso iwe ku dziko la makolo ako. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pambuyo pake Yakobe adauza Yosefe kuti, “Ukuwonatu kuti ndili pafupi kufa, koma Mulungu adzakhala nawe, ndipo adzakubweza ku dziko la makolo ako. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka Israeli anati kwa Yosefe, “Ine ndatsala pangʼono kufa, koma Mulungu adzakhala ndipo adzakutenganinso kubwerera nanu ku dziko la makolo anu. |
Ndipo Abramu anatenga Sarai mkazi wake, ndi Loti mwana wa mphwake, ndi chuma chao chimene anasonkhanitsa, ndi miyoyo imene anabala mu Harani; natuluka kunka ku dziko la Kanani, ndipo anadza ku dziko la Kanani.
ndiponso mtunduwo adzautumikira, Ine ndidzauweruza: ndiponso pambuyo pake adzatuluka ndi chuma chambiri.
Koma iwo adzabweranso kuno mbadwo wachinai: pakuti mphulupulu za Aamori sizinakwaniridwe.
khala mlendo m'dziko muno, ndipo Ine ndidzakhala ndi iwe, ndipo ndidzadalitsa iwe chifukwa kuti ndidzakupatsa iwe ndi mbeu zako maiko onse awa, ndipo ndidzalimbikitsa chilumbiriro ndinachilumbirira kwa Abrahamu atate wako;
Taonani, Ine ndili pamodzi ndi iwe, ndipo ndidzakusunga iwe konse kumene upitako, ndipo ndidzakubwezanso iwe ku dziko lino; chifukwa kuti sindidzakusiya iwe, kufikira kuti nditachita chimene ndanena nawe.
Ine ndidzatsikira pamodzi ndi iwe ku Ejipito; ndipo Ine ndidzakubwezanso ndithu; ndipo Yosefe adzaika dzanja lake pamaso pako.
Ndipo nthawi inayandikira kuti Israele adzafa, ndipo anaitana Yosefe mwana wake wamwamuna, nati kwa iye, Ngati ndapeza ufulu pamaso pako, ikatu dzanja lako pansi pa ntchafu yanga, nundichitire ine zabwino ndi zoona: usandiikatu ine mu Ejipito;
Yosefe ndipo anati kwa abale ake, Ndilinkufa ine, koma Mulungu adzaonekera kwa inu, adzakuchotsani inu m'dziko muno kubwera kunka ku dziko limene analumbirira kwa Abrahamu ndi kwa Isaki, ndi kwa Yakobo.
Yehova ngwa moyo; ndipo lidalitsike thanthwe langa; nakwezeke Mulungu wa chipulumutso changa.
Pakutitu, Davide, m'mene adautumikira uphungu wa Mulungu m'mbadwo mwake mwa iye yekha, anagona tulo, naikidwa kwa makolo ake, naona chivundi;
pamenepo Yehova Mulungu wanu adzauchotsa ukapolo wanu, ndi kukuchitirani chifundo; nadzabwera ndi kukumemezani mwa mitundu yonse ya anthu, kumene Yehova Mulungu wanu anakubalalitsiraniko.
Ndipo Yehova, Iye ndiye amene akutsogolera; Iye adzakhala ndi iwe, Iye sadzakusowa kapena kukusiya; usamachita mantha, usamatenga nkhawa.
wopanda atate wake, wopanda amake, wopanda mawerengedwe a chibadwidwe chake, alibe chiyambi cha masiku ake kapena chitsiriziro cha moyo wake, wofanizidwa ndi Mwana wa Mulungu), iyeyu wakhala wansembe kosalekeza.
Ndipo pano anthu ofeka alandira limodzi la magawo khumi; koma apo iye, woti adamchitira umboni kuti ali ndi moyo.
Palibe munthu adzatha kuima pamaso pako masiku onse a moyo wako; monga ndinakhala ndi Mose momwemo ndidzakhala ndi iwe; sindidzakusowa, sindidzakusiya.
Kodi sindinakulamulire iwe? Khala wamphamvu, nulimbike mtima, usaope, kapena kutenga nkhawa, pakuti Yehova Mulungu wako ali ndi iwe kulikonse umukako.
Ndipo taonani, lero lino ndilikumuka njira ya dziko lonse lapansi; ndipo mudziwa m'mitima yanu yonse, ndi m'moyo mwa inu nonse, kuti pa mau okoma onse Yehova Mulungu wanu anawanena za inu sanagwe padera mau amodzi; onse anachitikira inu, sanasowepo mau amodzi.
Ndipo Yehova anati kwa Yoswa, Lero lino ndidzayamba kukukuza pamaso pa Aisraele onse, kuti adziwe, kuti monga momwe ndinakhalira ndi Mose, momwemo ndidzakhala ndi iwe.
podziwa kuti kuleka kwa msasa wanga kuli pafupi, monganso Ambuye wathu Yesu Khristu anandilangiza.