Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Ahebri 7:3 - Buku Lopatulika

3 wopanda atate wake, wopanda amake, wopanda mawerengedwe a chibadwidwe chake, alibe chiyambi cha masiku ake kapena chitsiriziro cha moyo wake, wofanizidwa ndi Mwana wa Mulungu), iyeyu wakhala wansembe kosalekeza.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 wopanda atate wake, wopanda amake, wopanda mawerengedwe a chibadwidwe chake, alibe chiyambi cha masiku ake kapena chitsiriziro cha moyo wake, wofanizidwa ndi Mwana wa Mulungu), iyeyu wakhala wansembe kosalekeza.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Za bambo wake kapena mai wake, kapena makolo ake, palibe chilichonse chidalembedwa. Chimodzimodzi za kubadwa kwake ndi imfa yakenso. Ali ngati Mwana wa Mulungu, akupitiriza kukhala wansembe mpaka muyaya.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Alibe abambo kapena mayi, alibe chiyambi kapena chitsiriziro cha moyo wake. Iye ali ngati Mwana wa Mulungu ndipo akupitirira kukhala wansembe wamuyaya.

Onani mutuwo Koperani




Ahebri 7:3
11 Mawu Ofanana  

Ndi ana aamuna a Kohati ndiwo: Amuramu ndi Izihara, ndi Hebroni, ndi Uziyele; ndipo zaka za moyo wa Kohati ndizo zana limodzi ndi makumi atatu ndi kudza zitatu.


nasonkhanitsa khamu lonse tsiku loyamba la mwezi wachiwiri, ndipo iwo anawakumbira magwero ao kutchula mabanja ao, ndi nyumba za makolo ao, ndi kuwerenga maina kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu mmodzimmodzi.


Ndipo woyesayo anafika nanena kwa Iye, Ngati muli Mwana wa Mulungu, tauzani kuti miyala iyi isanduke mikate.


Popeza tsono tili naye Mkulu wa ansembe wamkulu, wopyoza miyamba, Yesu mwana wa Mulungu, tigwiritsitse chivomerezo chathu.


Pakuti Melkizedeki uyu, mfumu ya Salemu, wansembe wa Mulungu Wamkulukulu, amene anakomana ndi Abrahamu, pobwera iye adawapha mafumu aja, namdalitsa,


pakuti amchitira umboni, Iwe ndiwe wansembe nthawi yosatha monga mwa dongosolo la Melkizedeki.


amenenso Abrahamu anamgawira limodzi la magawo khumi la zonse (ndiye posandulika, poyamba ali mfumu ya chilungamo, pameneponso mfumu ya Salemu, ndiko, mfumu ya mtendere;


koma iye amene mawerengedwe a chibadwidwe chake sachokera mwa iwo, anatenga limodzi la magawo khumi kwa Abrahamu, namdalitsa iye amene ali nao malonjezano.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa