Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Ahebri 7:2 - Buku Lopatulika

2 amenenso Abrahamu anamgawira limodzi la magawo khumi la zonse (ndiye posandulika, poyamba ali mfumu ya chilungamo, pameneponso mfumu ya Salemu, ndiko, mfumu ya mtendere;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 amenenso Abrahamu anamgawira limodzi la magawo khumi la zonse (ndiye posandulika, poyamba ali mfumu ya chilungamo, pameneponso mfumu ya Salemu, ndiko, mfumu ya mtendere;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Abrahamu adampatsa chigawo chachikhumi cha zonse zimene adaafunkha. Potsata tanthauzo la dzina lake, choyamba Melkizedeki ndi “Mfumu ya chilungamo,” pambuyo pake ndi “Mfumunso ya Salemu,” ndiye kuti, “Mfumu ya Mtendere”.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Ndipo Abrahamu anamupatsa chakhumi cha zonse anafunkha. Choyamba dzina la Melikizedeki likutanthauza, “Mfumu ya chilungamo,” kenakanso, “Mfumu ya Salemu,” kutanthauza, “Mfumu ya mtendere.”

Onani mutuwo Koperani




Ahebri 7:2
26 Mawu Ofanana  

ndi mwala umenewu ndinauimiritsa, udzakhala nyumba ya Mulungu; ndipo la zonse mudzandipatsa ine, ndidzakupatsani Inu limodzi la magawo khumi.


Mulungu wa Israele anati, Thanthwe la Israele linalankhula ndi ine; kudzakhala woweruza anthu molungama; woweruza m'kuopa Mulungu.


Ndipo Davide anakhala mfumu ya Aisraele onse, Davide naweruza ndi chilungamo milandu ya anthu onse.


taona, udzabala mwana, ndiye adzakhala munthu wa phee; ndipo ndidzampumulitsira adani ake onse pozungulirapo, pakuti dzina lake lidzakhala Solomoni; ndipo ndidzapatsa Israele mtendere ndi bata masiku ake;


Masiku ake wolungama adzakhazikika; ndi mtendere wochuluka, kufikira sipadzakhala mwezi.


Ndipo limodzi la magawo khumi lonse la ng'ombe, kapena la nkhosa, kapena la mbuzi, zilizonse zimapita pansi pa ndodo, limodzi la magawo khumi likhala lopatulikira Yehova.


Ndipo ameneyo adzakhala mtendere; pamene a ku Asiriya adzalowa m'dziko lathu, ndi pamene adzaponda m'zinyumba zathu, tidzawaukitsira abusa asanu ndi awiri, ndi akalonga asanu ndi atatu.


Ndipo taonani, ndawaninkha ana a Levi limodzi la magawo khumi mwa zonse mu Israele, likhale cholowa chao, mphotho ya pa ntchito yao alikuichita, ntchito ya chihema chokomanako.


Onani namwali adzaima, nadzabala mwana wamwamuna, ndipo adzamutcha dzina lake, Imanuele. Ndilo losandulika, Mulungu nafe.


Ulemerero ukhale kwa Mulungu Kumwambamwamba, ndi mtendere pansi pano mwa anthu amene akondwera nao.


kuti aonetse chilungamo chake m'nyengo yatsopano; kuti Iye akhale wolungama, ndi wakumuyesa wolungama iye amene akhulupirira Yesu.


Pakuti Melkizedeki uyu, mfumu ya Salemu, wansembe wa Mulungu Wamkulukulu, amene anakomana ndi Abrahamu, pobwera iye adawapha mafumu aja, namdalitsa,


wopanda atate wake, wopanda amake, wopanda mawerengedwe a chibadwidwe chake, alibe chiyambi cha masiku ake kapena chitsiriziro cha moyo wake, wofanizidwa ndi Mwana wa Mulungu), iyeyu wakhala wansembe kosalekeza.


Ndipo idzatenga limodzi la magawo khumi la mbeu zanu, ndi la minda yanu yampesa, nidzalipatsa akapitao ake, ndi anyamata ake.


Idzatenga limodzi la magawo khumi la zoweta zanu; ndipo inu mudzakhala akapolo ake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa