Ahebri 7:1 - Buku Lopatulika1 Pakuti Melkizedeki uyu, mfumu ya Salemu, wansembe wa Mulungu Wamkulukulu, amene anakomana ndi Abrahamu, pobwera iye adawapha mafumu aja, namdalitsa, Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20141 Pakuti Melkizedeki uyu, mfumu ya Salemu, wansembe wa Mulungu Wamkulukulu, amene anakomana ndi Abrahamu, pobwera iye adawapha mafumu aja, namdalitsa, Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa1 Melkizedeki ameneyu anali mfumu ya ku Salemu, ndiponso wansembe wa Mulungu Wopambanazonse. Pamene Abrahamu ankabwerako kuchokera ku nkhondo, atagonjetsa mafumu aja, Melkizedeki adadzamchingamira, namdalitsa. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero1 Melikizedeki ameneyu anali mfumu ya ku Salemu, ndiponso wansembe wa Mulungu Wammwambamwamba. Anakumana ndi Abrahamu pamene ankabwerera kuchokera ku nkhondo atagonjetsa mafumu aja, Melikizedeki anakumana naye namudalitsa. Onani mutuwo |
ndipo anamuinga kumchotsa kwa ana a anthu, ndi mtima wake unasandulika ngati wa nyama zakuthengo, ndi pokhala pake mpa mbidzi, anamdyetsa udzu ngati ng'ombe, ndi thupi lake linakhathamira ndi mame a kumwamba; mpaka anadziwa kuti Wam'mwambamwamba alamulira mu ufumu wa anthu, nauikira aliyense Iye afuna mwini.