Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 47:29 - Buku Lopatulika

29 Ndipo nthawi inayandikira kuti Israele adzafa, ndipo anaitana Yosefe mwana wake wamwamuna, nati kwa iye, Ngati ndapeza ufulu pamaso pako, ikatu dzanja lako pansi pa ntchafu yanga, nundichitire ine zabwino ndi zoona: usandiikatu ine mu Ejipito;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

29 Ndipo nthawi inayandikira kuti Israele adzafa, ndipo anaitana Yosefe mwana wake wamwamuna, nati kwa iye, Ngati ndapeza ufulu pamaso pako, ikatu dzanja lako pansi pa ntchafu yanga, nundichitire ine zabwino ndi zoona: usandiikatu ine m'Ejipito;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

29 Tsono ali pafupi kumwalira, adaitana mwana wake Yosefe namuuza kuti, “Ngati ukundikondadi, undigwire m'kati mwa ntchafu zangazi, ulonjeze kuti udzandikomera mtima ndi kukhulupirika kwa ine, ndipo kuti mtembo wanga sudzauika ku Ejipito kuno.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

29 Nthawi itayandikira yoti Israeli amwalire, anayitanitsa mwana wake Yosefe nati kwa iye, “Ngati ukundikondadi monga abambo ako, ika dzanja lako pansi pa ntchafu yanga ndipo ulonjeze kuti udzaonetsa kukoma mtima ndi kukhulupirika kwako kwa ine kuti sudzayika mtembo wanga kuno ku Igupto.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 47:29
28 Mawu Ofanana  

Ndipo Abrahamu anati kwa mnyamata wake wamkulu wa pa nyumba yake, amene analamulira pa zonse anali nazo, Taikatu dzanja lako pansi pa ntchafu yanga:


Tsopano, ngati mudzamchitira mbuyanga zaufulu ndi zoonadi, mundiuze, ngati iai, mundiuze; kuti ndipatukire ku dzanja lamanja kapena ku dzanja lamanzere.


Ndipo anati, Taonatu, ndakalamba, sindidziwa tsiku la kufa kwanga:


m'thukuta la nkhope yako udzadya chakudya, kufikira kuti udzabwerera kunthaka: chifukwa kuti m'menemo unatengedwa: chifukwa kuti ndiwe fumbi, ndi kufumbiko udzabwerera.


Ndipo Yakobo anati kwa Farao, Masiku a zaka za ulendo wanga ndi zaka zana limodzi kudza makumi atatu; masiku a zaka za moyo wanga ali owerengeka ndi oipa, sanafikire masiku a zaka za moyo wa makolo anga m'masiku a ulendo wao.


Ndipo Israele anati kwa Yosefe, Taona, ndilinkufa ine; Mulungu adzakhala ndi iwe, adzakubwezanso iwe ku dziko la makolo ako.


Ndipo ana ake aamuna anamchitira iye monga anawalamulira iwo;


Atate wanga anandilumbiritsa ine, kuti, Taona, ndilinkufa; m'manda m'mene ndadzikonzeratu ndekha m'dziko la Kanani, m'menemo udzandiika ine. Tsopano mundiloletu, ndikwereko, ndipite, ndikaike atate wanga, nditatero ndidzabweranso.


Pakuti kufa tidzafa, ndipo tili ngati madzi otayika pansi amene sangathe kuwaolanso; ngakhale Mulungu sachotsa moyo, koma alingalira njira yakuti wotayikayo asakhale womtayikira Iye.


Ndipo ananyamula Asahele namuika m'manda a atate wake ali ku Betelehemu. Ndipo Yowabu ndi anthu ake anachezera kuyenda usiku wonse, ndipo kudawachera ku Hebroni.


Pamene masiku ako akadzakwaniridwa, ndipo iwe udzagona ndi makolo ako, Ine ndidzaukitsa mbeu yako pambuyo pako, imene idzatuluka m'matumbo mwako, ndipo ndidzakhazikitsa ufumu wake.


Pakuyandikira masiku ake a Davide akuti amwalire, analamulira Solomoni mwana wake, nati,


Atafa munthu, adzakhalanso ndi moyo kodi? Ndikadayembekeza masiku onse a nkhondo yanga, mpaka kwafika kusandulika kwanga.


Pakuti ndidziwa kuti mudzandifikitsa kuimfa, ndi kunyumba yokomanamo amoyo onse.


Kodi munthu alibe nkhondo kunja kuno? Kodi masiku ake sakunga masiku a wolembedwa ntchito?


kuombola mbale sangadzamuombole, kapena kumperekera dipo kwa Mulungu.


Kuti akhale ndi moyo osafa, osaona chivundi.


Pakuti muimfa m'mosakumbukira Inu; m'mandamo adzakuyamikani ndani?


Munthu ndani amene adzakhalabe ndi moyo, osaona imfa? Amene adzapulumutsa moyo wake kumphamvu ya manda?


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Taona, ayandikira masiku ako akuti uyenera kufa; kaitane Yoswa, nimuoneke m'chihema chokomanako, kuti ndimlangize. Namuka Mose ndi Yoswa, naoneka m'chihema chokomanako.


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Taona, udzagona tulo ndi makolo ako; ndi anthu awa adzauka, nadzatsata ndi chigololo milungu yachilendo ya dziko limene analowa pakati pake, nadzanditaya Ine, ndi kuthyola chipangano changa ndinapangana naocho.


Ndi chikhulupiriro, Yosefe, pakumwalira, anatchula za matulukidwe a ana a Israele; nalamulira za mafupa ake.


Ndipo popeza kwaikikatu kwa anthu kufa kamodzi, ndipo atafa, chiweruziro;


Ndipo amunawo anati kwa iye, Moyo wathu ndiwo moyo wanu, mukapanda kuwulula chodzera ife; ndipo kudzakhala kuti, pakutipatsa ife dziko ili Yehova, tidzakuchitira chifundo ndi choonadi.


Ndipo taonani, lero lino ndilikumuka njira ya dziko lonse lapansi; ndipo mudziwa m'mitima yanu yonse, ndi m'moyo mwa inu nonse, kuti pa mau okoma onse Yehova Mulungu wanu anawanena za inu sanagwe padera mau amodzi; onse anachitikira inu, sanasowepo mau amodzi.


Nati Davide, Pali Yehova, Yehova adzamkantha iye; kapena tsiku la imfa yake lidzafika; kapena adzatsikira kunkhondo, nadzafako.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa