Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 47:30 - Buku Lopatulika

30 koma pamene ndidzagona ndi makolo anga, udzanditenge ine kutuluka m'dziko la Ejipito, ukandiike ine m'manda mwao. Ndipo iye anati, Ndidzachita monga mwanena.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

30 koma pamene ndidzagona ndi makolo anga, udzanditenge ine kutuluka m'dziko la Ejipito, ukandiike ine m'manda mwao. Ndipo iye anati, Ndidzachita monga mwanena.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

30 Ndifuna kukagona pamodzi ndi makolo anga. Mtembo wanga udzauchotse ku Ejipito kuno ukauike m'manda a makolo anga.” Yosefe adayankha kuti, “Ndidzachita monga momwe mwaneneramu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

30 Ine ndikagona pamodzi ndi makolo anga. Choncho ndikadzamwalira udzanditulutse mu Igupto muno ndipo ukayike mtembo wanga kumene anayikidwa makolo anga.” Yosefe anati, “Ndidzachita monga mwanenera.”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 47:30
16 Mawu Ofanana  

Ndipo iwe udzanka kwa makolo ako m'mtendere; nudzaikidwa ndi ukalamba wabwino.


Ndipo munda wa Efuroni umene unali mu Makipela, umene unali patsogolo pa Mamure, munda ndi phanga lili momwemo, ndi mitengo yonse inali m'mundamo, yokhala m'malire monse mozungulira momwemo,


Zitatha izi Abrahamu anaika Sara mkazi wake m'phanga la munda wa Makipela patsogolo pa Mamure (ndiwo Hebroni), m'dziko la Kanani.


munda umene anagula Abrahamu kwa ana a Hiti. Pamenepo anamuika Abrahamu ndi Sara mkazi wake.


Ndipo ana ake Isaki ndi Ismaele anamuika iye m'phanga la Makipela, m'munda wa Efuroni mwana wake wa Zohari Muhiti, umene uli patsogolo pa Mamure;


Ndipo Isaki anatsirizika nafa, nasonkhanitsidwa kwa anthu a mtundu wake, wokalamba ndi wa masiku okwanira: ndipo Esau ndi Yakobo ana ake aamuna anamuika iye.


Ndipo Yosefe analumbiritsa ana a Israele kuti, Mulungu adzaonekera kwa inu ndithu, ndipo mudzakwera nao mafupa anga kuchokera kuno.


Mulole mnyamata wanu ndibwererenso, kuti ndikamwalire m'mzinda wanga kumanda a atate wanga ndi mai wanga. Koma suyu, Kimuhamu mnyamata wanu, iye aoloke pamodzi ndi mbuye wanga mfumu, ndipo mumchitire chimene chikukomerani.


Ndipo ananyamula Asahele namuika m'manda a atate wake ali ku Betelehemu. Ndipo Yowabu ndi anthu ake anachezera kuyenda usiku wonse, ndipo kudawachera ku Hebroni.


koma unabwerera nudya mkate, ndi kumwa madzi paja pomwe Iye anakuuza, Usakadye mkate, kapena kumwa madzi, mtembo wako tsono sudzaikidwa ku manda a atate ako.


Ndipo ndinati kwa mfumu, Mfumu ikhale ndi moyo kosatha; ilekerenji nkhope yanga kuchita chisoni, popeza pali bwinja kumzinda kuli manda a makolo anga, ndi zipata zake zopsereza ndi moto.


Ndipo ndinati kwa mfumu, Chikakomera mfumu, ndi mtima wanu ukakomera kapolo wanu, munditumize ku Yuda kumzinda wa manda a makolo anga, kuti ndiumange.


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Taona, udzagona tulo ndi makolo ako; ndi anthu awa adzauka, nadzatsata ndi chigololo milungu yachilendo ya dziko limene analowa pakati pake, nadzanditaya Ine, ndi kuthyola chipangano changa ndinapangana naocho.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa