Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yoswa 3:7 - Buku Lopatulika

7 Ndipo Yehova anati kwa Yoswa, Lero lino ndidzayamba kukukuza pamaso pa Aisraele onse, kuti adziwe, kuti monga momwe ndinakhalira ndi Mose, momwemo ndidzakhala ndi iwe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ndipo Yehova anati kwa Yoswa, Lero lino ndidzayamba kukukuza pamaso pa Aisraele onse, kuti adziwe, kuti monga momwe ndinakhalira ndi Mose, momwemo ndidzakhala ndi iwe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Apo Chauta adauza Yoswa kuti, “Zimene ndikuchita lerozi, ndizo zidzapatse Aisraele onse mtima wokulemekeza iwe, kuti ndiwe munthu wamkulu. Ndipo adzadziŵa kuti Ine ndili nawe monga momwe ndidakhalira ndi Mose.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Ndipo Yehova anati kwa Yoswa, “Lero Ine ndidzayamba kukukweza pamaso pa Aisraeli onse kuti adziwe kuti ndili nawe monga ndinalili ndi Mose.

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 3:7
13 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova anakuza Solomoni kwakukulu pamaso pa Aisraele onse, nampatsa ulemerero wachifumu, wakuti, asanakhale iyeyu, panalibe mfumu ya Israele inali nao wotero.


Ndipo Solomoni mwana wa Davide analimbikitsidwa mu ufumu wake, ndipo Yehova Mulungu wake anali naye, namkuza kwakukulu.


Munthu ndani kuti mumkuze, ndi kuti muike mtima wanu pa iye,


Ndipo mwandipatsa chikopa cha chipulumutso chanu; ndipo dzanja lamanja lanu landigwiriziza, ndipo chifatso chanu chandikuza ine.


Zinthu izi analankhula Yesu; ndipo m'mene anakweza maso ake Kumwamba, anati, Atate, yafika nthawi; lemekezani Mwana wanu, kuti Mwana wanu akulemekezeni Inu;


monga mwa kulingiriritsa ndi chiyembekezo changa, kuti palibe chinthu chidzandichititsa manyazi, komatu mwa kulimbika mtima konse, monga nthawi yonse, tsopanonso Khristu adzakuzidwa m'thupi langa, kapena mwa moyo, kapena mwa imfa.


Monga momwe tinamvera mau onse a Mose momwemo tidzamvera inu; komatu akhale ndi inu Yehova Mulungu wanu monga anakhala ndi Mose.


Palibe munthu adzatha kuima pamaso pako masiku onse a moyo wako; monga ndinakhala ndi Mose momwemo ndidzakhala ndi iwe; sindidzakusowa, sindidzakusiya.


Kodi sindinakulamulire iwe? Khala wamphamvu, nulimbike mtima, usaope, kapena kutenga nkhawa, pakuti Yehova Mulungu wako ali ndi iwe kulikonse umukako.


Ndipo Yoswa anati kwa ansembe, Senzani likasa la chipangano, nimuoloke pamaso pa anthu. Nasenza iwo likasa la chipangano, natsogolera anthu.


Ndipo uzilamulira ansembe akunyamula likasa la chipangano, ndi kuti, Pamene mufika kumphepete kwa madzi a Yordani muziima mu Yordani.


Tsiku lomwelo Yehova anakulitsa Yoswa pamaso pa Aisraele onse; ndipo anamuopa monga anaopa Mose, masiku onse a moyo wake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa