Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Timoteyo 4:6 - Buku Lopatulika

6 Pakuti ndilimkuthiridwa nsembe tsopano, ndipo nthawi ya kumasuka kwanga yafika.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Pakuti ndilimkuthiridwa nsembe tsopano, ndipo nthawi ya kumasuka kwanga yafika.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Paja ine ndiye moyo wanga wayamba kale kuthiridwa ngati nsembe, ndipo nthaŵi yafika kuti ndinyamuke ulendo wanga wochoka m'moyo uno.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Pakuti moyo wanga wayamba kale kuthiridwa ngati nsembe, ndipo nthawi yakwana yoti ndinyamuke ulendo wanga.

Onani mutuwo Koperani




2 Timoteyo 4:6
8 Mawu Ofanana  

Ndipo Israele anati kwa Yosefe, Taona, ndilinkufa ine; Mulungu adzakhala ndi iwe, adzakubwezanso iwe ku dziko la makolo ako.


Yosefe ndipo anati kwa abale ake, Ndilinkufa ine, koma Mulungu adzaonekera kwa inu, adzakuchotsani inu m'dziko muno kubwera kunka ku dziko limene analumbirira kwa Abrahamu ndi kwa Isaki, ndi kwa Yakobo.


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Taona, ayandikira masiku ako akuti uyenera kufa; kaitane Yoswa, nimuoneke m'chihema chokomanako, kuti ndimlangize. Namuka Mose ndi Yoswa, naoneka m'chihema chokomanako.


Koma ndipanidwa nazo ziwirizi, pokhala nacho cholakalaka cha kuchoka kukhala ndi Khristu, ndiko kwabwino koposaposatu;


Komatu ngatinso ndithiridwa pa nsembe ndi kutumikira kwa chikhulupiriro chanu, ndikondwera, ndipo ndikondwera pamodzi ndi inu nonse;


Ndipo taonani, lero lino ndilikumuka njira ya dziko lonse lapansi; ndipo mudziwa m'mitima yanu yonse, ndi m'moyo mwa inu nonse, kuti pa mau okoma onse Yehova Mulungu wanu anawanena za inu sanagwe padera mau amodzi; onse anachitikira inu, sanasowepo mau amodzi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa