Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 13:36 - Buku Lopatulika

36 Pakutitu, Davide, m'mene adautumikira uphungu wa Mulungu m'mbadwo mwake mwa iye yekha, anagona tulo, naikidwa kwa makolo ake, naona chivundi;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

36 Pakutitu, Davide, m'mene adautumikira uphungu wa Mulungu m'mbadwo mwake mwa iye yekha, anagona tulo, naikidwa kwa makolo ake, naona chivundi;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

36 Paja Davide adati atakwaniritsa zimene Mulungu adaakonzeratu pa masiku a mbadwo wake, adamwalira naikidwa m'manda pamodzi ndi makolo ake, ndipo thupi lake lidaola.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

36 “Pakuti pamene Davide anatsiriza kutumikira Mulungu mu mʼbado wake, anamwalira, iye anayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake ndipo thupi lake linawola.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 13:36
33 Mawu Ofanana  

m'thukuta la nkhope yako udzadya chakudya, kufikira kuti udzabwerera kunthaka: chifukwa kuti m'menemo unatengedwa: chifukwa kuti ndiwe fumbi, ndi kufumbiko udzabwerera.


Pamene masiku ako akadzakwaniridwa, ndipo iwe udzagona ndi makolo ako, Ine ndidzaukitsa mbeu yako pambuyo pako, imene idzatuluka m'matumbo mwako, ndipo ndidzakhazikitsa ufumu wake.


Ndipo Davide anagona pamodzi ndi makolo ake, naikidwa m'mzinda wa Davide.


Ngakhale kale lomwe, pokhala mfumu Sauloyo, wotuluka ndi kulowa nao Aisraele ndinu; ndipo Yehova Mulungu wanu anati kwa inu, Uzidyetsa anthu anga Aisraele, nukhale mtsogoleri wa anthu anga Israele.


Ndipo kudzachitika, atakwanira masiku ako kuti uzipita kukhala ndi makolo ako, ndidzaukitsa mbeu yako pambuyo pako, ndiye wa ana ako; ndipo ndidzakhazikitsa ufumu wake.


Ndipo Davide anakhala mfumu ya Aisraele onse, naweruza anthu ake onse, nawachitira chilungamo.


Nafa atakalamba bwino, wochuluka masiku, zolemera, ndi ulemerero; ndi Solomoni mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.


Nagona Rehobowamu ndi makolo ake, naikidwa m'mzinda wa Davide; ndipo Abiya mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.


Ndipo Yehosafati anagona pamodzi ndi makolo ake, naikidwa pamodzi ndi makolo ake m'mzinda wa Davide; ndi Yehoramu mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.


Ndipo Uziya anagona ndi makolo ake, namuika ndi makolo ake kumanda kwa mafumu; pakuti anati, Ndiye wakhate; ndi Yotamu mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.


Nagona Solomoni pamodzi ndi makolo ake, naikidwa m'mzinda wa Davide atate wake; ndipo Rehobowamu mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.


Ndikati kwa dzenje, Ndiwe atate wanga; kwa mphutsi, Ndiwe mai wanga ndi mlongo wanga;


Iwo agona chimodzimodzi kufumbi, ndi mphutsi ziwakuta.


Aikidwa m'manda ngati nkhosa; mbusa wao ndi imfa. Ndipo m'mawa mwake oongoka mtima adzakhala mafumu ao; ndipo maonekedwe ao adzanyekera kumanda, kuti pokhala pake padzasowa.


Kuti akhale ndi moyo osafa, osaona chivundi.


Pomwepo uyo amene analandira matalente asanu, anapita kugula nazo malonda, napindulapo matalente ena asanu.


Yesu ananena, Chotsani mwala. Marita, mlongo wake wa womwalirayo, ananena ndi Iye, Ambuye, adayamba kununkha: pakuti wagona masiku anai.


Ndipo m'mene atamchotsa iye, anawautsira Davide akhale mfumu yao; amenenso anamchitira umboni, nati, Ndapeza Davide, mwana wa Yese, munthu wa pamtima panga, amene adzachita chifuniro changa chonse.


Amuna inu, abale, kuloleka kunena poyera posaopa kwa inu za kholo lija Davide, kuti adamwalira naikidwanso, ndipo manda ake ali ndi ife kufikira lero lino.


Pakuti sindinakubisirani pakukulalikirani uphungu wonse wa Mulungu.


Ndipo m'mene anagwada pansi, anafuula ndi mau aakulu, Ambuye, musawaikire iwo tchimo ili. Ndipo m'mene adanena ichi, anagona tulo.


Ndipo Saulo analikuvomerezana nao pa imfa yake. Ndipo tsikulo kunayamba kuzunza kwakukulu pa Mpingo unali mu Yerusalemu; ndipo anabalalitsidwa onse m'maiko a Yudeya ndi Samariya, koma osati atumwi ai.


Chifukwa chake iwonso akugona mwa Khristu anatayika.


pomwepo anaoneka pa nthawi imodzi kwa abale oposa mazana asanu, amene ochuluka a iwo akhala kufikira tsopano, koma ena agona;


Koma sitifuna, abale, kuti mukhale osadziwa za iwo akugona; kuti mungalire monganso otsalawo, amene alibe chiyembekezo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa