Mulungu ndipo anadalitsa iwo, ndipo adati kwa iwo, Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pansomba za m'nyanja, ndi pambalame za m'mlengalenga, ndi pazamoyo zonse zokwawa padziko lapansi.
Genesis 28:3 - Buku Lopatulika Mulungu Wamphamvuyonse akudalitse iwe, akubalitse iwe, akuchulukitse iwe, kuti ukhale khamu la anthu: Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mulungu Wamphamvuyonse akudalitse iwe, akubalitse iwe, akuchulukitse iwe, kuti ukhale khamu la anthu: Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mulungu Mphambe adalitse ukwati wako, ndipo akupatse ana ochuluka, kuti udzakhale gulu lalikulu la mitundu yambiri ya anthu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mulungu Wamphamvuzonse akudalitse iwe nakupatse ana ambiri mpaka udzasanduke gulu lalikulu la mitundu ya anthu. |
Mulungu ndipo anadalitsa iwo, ndipo adati kwa iwo, Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pansomba za m'nyanja, ndi pambalame za m'mlengalenga, ndi pazamoyo zonse zokwawa padziko lapansi.
Ndipo ndidzayesa mbeu yako monga fumbi lapansi: chotere kuti ngati munthu angathe kuwerenga fumbi lapansi, chomwechonso mbeu yako idzawerengedwa.
Koma za Ismaele, ndamvera iwe: taona, ndamdalitsa iye, ndipo ndidzamchulukitsa iye ndithu; adzabala akalonga khumi ndi awiri, ndipo ndidzamuyesa iye mtundu waukulu.
Ndipo anamdalitsa Rebeka, nati kwa iye, Mlongo wathu ndiwe, iwe ukhale amai wa anthu zikwizikwi, mbeu zako zigonjetse chipata cha iwo akudana nao.
Ndipo Yehova anamuonekera iye usiku womwewo, nati, Ine ndine Mulungu wa Abrahamu atate wako; usaope, chifukwa kuti Ine ndili ndi iwe, ndipo ndidzakudalitsa iwe, ndi kuchulukitsa mbeu zako, chifukwa cha Abrahamu kapolo wanga.
ndipo ndidzachulukitsa mbeu zako monga nyenyezi za kumwamba, ndipo ndidzapatsa mbeu zako maiko onsewa; m'mbeu zako mitundu yonse ya dziko lapansi idzadalitsidwa;
Ndipo Isaki ananthunthumira ndi kunthunthumira kwakukulu, nati, Ndani uja anatenga nyama, nadza nayo kwa ine, ndipo ndadyako zonse usadalowe iwe, ndipo ndamdalitsa iye? Inde, adzadalitsika.
Ndipo Mulungu anati kwa iye, Ine ndine Mulungu Wamphamvuyonse: ubale, uchuluke; mwa iwe mudzatuluka mtundu ndi gulu la mitundu, ndipo mafumu adzatuluka m'chuuno mwako;
Ndipo dzina la wachiwiri anamutcha Efuremu: chifukwa Mulungu anandibalitsa ine m'dziko la kusauka kwanga.
Mulungu Wamphamvuyonse adzakupatsani inu chifundo pamaso pa munthu uja, kuti akumasulireni inu mbale wanu wina ndi Benjamini. Ndipo ine, ngati ndikhala wopanda ana, ndikhalatu.
Ndipo Yakobo anati kwa Yosefe, Mulungu Wamphamvuyonse anaonekera kwa ine pa Luzi m'dziko la Kanani nandidalitsa ine, nati kwa ine,
Taona, ndidzakubalitsa iwe, ndidzakuchulukitsa iwe, ndidzakusandutsa iwe khamu la anthu a mitundu; ndipo ndidzapatsa mbeu yako ya pambuyo pako dziko ili likhale laolao chikhalire.
Ndi Mulungu wa atate wako amene adzakuthangata iwe, ndi Wamphamvuyonse, amene adzakudalitsa iwe. Ndi madalitso a Kumwamba, madalitso a madzi akuya akukhala pansi, madalitso a mawere, ndi a mimba.
Ndipo Mulungu anadalitsa Nowa ndi ana ake, nati kwa iwo, Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi.
Akapanda kumanga nyumba Yehova, akuimanga agwiritsa ntchito chabe; akapanda kusunga mzinda Yehova, mlonda adikira chabe.
Ana a Israele ndipo anaswana, nabalana, nachuluka, nakhala nazo mphamvu zazikulu; ndipo dziko linadzala nao.
ndipo ndinaonekera Abrahamu, Isaki ndi Yakobo, Mulungu Wamphamvuyonse; koma sindinadziwike kwa iwo ndi dzina langa YEHOVA.
ndipo ndidzakhala kwa inu Atate, ndi inu mudzakhala kwa Ine ana aamuna ndi aakazi, anena Ambuye Wamphamvuyonse.
Ndipo sindinaone Kachisi momwemo; pakuti Ambuye Mulungu Wamphamvuyonse, ndi Mwanawankhosa ndiwo Kachisi wake.
Ndipo taona, Bowazi anafuma ku Betelehemu, nati kwa ocheka, Yehova akhale nanu. Namyankha iwo, Yehova akudalitseni.