Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 24:60 - Buku Lopatulika

60 Ndipo anamdalitsa Rebeka, nati kwa iye, Mlongo wathu ndiwe, iwe ukhale amai wa anthu zikwizikwi, mbeu zako zigonjetse chipata cha iwo akudana nao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

60 Ndipo anamdalitsa Rebeka, nati kwa iye, Mlongo wathu ndiwe, iwe ukhale amai wa anthu zikwizikwi, mbeu zako zigonjetse chipata cha iwo akudana nao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

60 Ndipo adamdalitsa Rebekayo ponena mau akuti, “Iwe mwana wathu, Chauta akudalitse kuti udzakhale mai wa anthu zikwi zambirimbiri. Zidzukulu zako zidzagonjetse mizinda ya adani ao.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

60 Ndipo iwo anadalitsa Rebeka ndi kumuwuza kuti, “Iwe ndiwe mlongo wathu, Mulungu akudalitse iwe, ukhale mayi wa anthu miyandamiyanda; ndi kuti zidzukulu zako zidzalanda mizinda ya adani awo.”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 24:60
15 Mawu Ofanana  

Mulungu ndipo anadalitsa iwo, ndipo adati kwa iwo, Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pansomba za m'nyanja, ndi pambalame za m'mlengalenga, ndi pazamoyo zonse zokwawa padziko lapansi.


Ndipo anamdalitsa iye, nati, Abramu adalitsike ndi Mulungu Wamkulukulu, mlengi wa kumwamba ndi dziko lapansi;


Ndipo ndidzamdalitsa iye, ndiponso ndidzakupatsa iwe mwana wamwamuna wobadwa mwa iye, inde, ndidzamdalitsa iye, ndipo adzakhala amake amitundu, mafumu a anthu adzatuluka mwa iye.


kudalitsa ndidzakudalitsa iwe, kuchulukitsa ndidzachulukitsa mbeu zako monga nyenyezi za kumwamba, monga mchenga wa m'mphepete mwa nyanja; ndipo mbeu zako zidzagonjetsa chipata cha adani ao;


Ndipo adauka Rebeka ndi anamwali ake, nakwera pa ngamira natsata munthuyo: mnyamatayo ndipo anamtenga Rebeka namuka.


Mulungu Wamphamvuyonse akudalitse iwe, akubalitse iwe, akuchulukitse iwe, kuti ukhale khamu la anthu:


Ndipo Yakobo anankabe ulendo wake, ndipo amithenga a Mulungu anakomana naye.


Ndipo anadalitsa iwo tsiku lomwelo, nati, Mwa iwe Israele adzadalitsa, kuti, Mulungu akuyese iwe monga Efuremu ndi monga Manase; ndipo anaika Efuremu woyamba wa Manase.


Ndipo Mulungu anadalitsa Nowa ndi ana ake, nati kwa iwo, Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi.


tengani akazi, balani ana aamuna ndi aakazi; kwatitsani ana anu aamuna, patsani ananu aakazi kwa amuna, kuti abale ana aamuna ndi aakazi; kuti mubalane pamenepo musachepe.


Mtsinje wamoto unayenda wotuluka pamaso pake, zikwizikwi anamtumikira, ndi unyinji wosawerengeka unaima pamaso pake, woweruza mlandu anakhalapo, ndi mabuku anatsegulidwa.


Ndipo muwayese cholowa cha ana anu akudza m'mbuyo, akhale aoao; muwayese akapolo kosatha; koma za abale anu, ana a Israele, musamalamulirana mozunza.


azimgwira atate wake ndi mai wake, ndi kutulukira naye kwa akulu a mzinda wake, ndi ku chipata cha malo ake;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa