Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 27:33 - Buku Lopatulika

33 Ndipo Isaki ananthunthumira ndi kunthunthumira kwakukulu, nati, Ndani uja anatenga nyama, nadza nayo kwa ine, ndipo ndadyako zonse usadalowe iwe, ndipo ndamdalitsa iye? Inde, adzadalitsika.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

33 Ndipo Isaki ananthunthumira ndi kunthunthumira kwakukulu, nati, Ndani uja anatenga nyama, nadza nayo kwa ine, ndipo ndadyako zonse usadalowe iwe, ndipo ndamdalitsa iye? Inde, adzadalitsika.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

33 Pompo Isaki adayamba kunjenjemera thupi lonse, nafunsa kuti, “Nanga uja adapha nyama nkubwera nayo kwa ineyu ndani? Ndadya kale imeneyo, iwe usanabwere. Ndamudalitsa kale, ndipo madalitso amenewo ndi ake mpaka muyaya.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

33 Isake ananjenjemera kwambiri nati, “Nanga ndani uja anakapha nyama kutchire nʼkudzandipatsa? Ine ndadya kale, ndadya nyamayo iwe utangotsala pangʼono kubwera ndipo ndamudalitsa ndipo adzakhaladi wodalitsika.”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 27:33
14 Mawu Ofanana  

Yehova ndipo anati kwa iye, Mitundu iwiri ili m'mimba mwako, magulu awiri a anthu adzatuluka m'mimba mwako; gulu lina lidzapambana mphamvu ndi linzake; wamkulu adzakhala kapolo wa wamng'ono.


Ndipo iye anati, Mphwako anadza monyenga, nalanda mdalitso wako.


Ndipo Isaki anamuitana Yakobo, namdalitsa iye, namuuza iye, nati kwa iye, Usatenge mkazi wa ana aakazi a Kanani.


Ndikangokumbukira ndivutika mtima, ndi thupi langa lichita nyaunyau.


Pa ichinso mtima wanga unjenjemera, nusunthika m'malo mwake.


Mantha ndi kunjenjemera zandidzera, ndipo zoopsetsa zandikuta.


Kapena kulankhula, osachitsimikiza? Taonani, ndalandira mau akudalitsa, popeza Iye wadalitsa, sinditha kusintha.


Siikudza mbala, koma kuti ikabe, ndi kupha, ndi kuononga. Ndadza Ine kuti akhale ndi moyo, ndi kukhala nao wochuluka.


Pakuti mphatso zake ndi kuitana kwake kwa Mulungu sizilapika.


Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, amene anatidalitsa ife ndi dalitso lonse la mzimu m'zakumwamba mwa Khristu;


Ndi chikhulupiriro Isaki anadalitsa Yakobo ndi Esau, zingakhale za zinthu zilinkudza.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa