Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 41:52 - Buku Lopatulika

52 Ndipo dzina la wachiwiri anamutcha Efuremu: chifukwa Mulungu anandibalitsa ine m'dziko la kusauka kwanga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

52 Ndipo dzina la wachiwiri anamutcha Efuremu: chifukwa Mulungu anandibalitsa ine m'dziko la kusauka kwanga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

52 Ndipo adanenanso kuti, “Mulungu wandipatsa ana m'dziko la masautso anga.” Motero mwana wachiŵiriyo adamutcha Efuremu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

52 Mwana wachiwiri wa mwamuna anamutcha Efereimu popeza anati, “Mulungu wandipatsa ana mʼdziko la masautso anga.”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 41:52
21 Mawu Ofanana  

Ndipo ndikubalitsa iwe ndithu, ndipo ndidzakuyesa iwe mitundu, ndipo mafumu adzatuluka mwa iwe.


Mulungu Wamphamvuyonse akudalitse iwe, akubalitse iwe, akuchulukitse iwe, kuti ukhale khamu la anthu:


Ndipo Yosefe anamutcha dzina la woyamba Manase, chifukwa anati iye, Mulungu wandiiwalitsa ine zovuta zanga zonse, ndi nyumba yonse ya atate wanga.


Ndipo zaka zakuchuluka dzinthu zisanu ndi ziwiri za m'dziko la Ejipito, zinatha.


Ndipo panali zitapita izi, anthu anati kwa Yosefe, Taonani, atate wanu wadwala: ndipo iye anatenga ana ake aamuna awiri, Manase ndi Efuremu, apite naye.


Ndipo Israele anatambalitsa dzanja lake lamanja, naliika pamutu wa Efuremu, amene ndiye wamng'ono, ndi dzanja lake lamanzere pamutu wa Manase, anapingasitsa manja ake dala; chifukwa Manase anali woyamba.


Tsopano ana ako aamuna awiri, amene anakubadwira iwe m'dziko la Ejipito, ndisanadze kwa iwe ku Ejipito, ndiwo anga; Efuremu ndi Manase, monga Rubeni ndi Simeoni, ndiwo anga.


Yosefe ndi nthambi yobala, nthambi yobala pambali pa kasupe; nthambi zake ziyangayanga palinga.


Ndipo Yosefe anaona ana a Efuremu a mbadwo wachitatu; ananso a Makiri mwana wamwamuna wa Manase anabadwa pa maondo a Yosefe.


akumwera vinyo m'zipanda, nadzidzoza ndi mafuta abwino oposa, osagwidwa chisoni ndi kuthyoka kwa Yosefe.


Ana aamuna a Yosefe monga mwa mabanja ao ndiwo: Manase ndi Efuremu.


namlanditsa iye m'zisautso zake zonse, nampatsa chisomo ndi nzeru pamaso pa Farao mfumu ya ku Ejipito; ndipo anamuika iye kazembe wa pa Ejipito ndi pa nyumba yake yonse.


Pakuti ana a Yosefe ndiwo mafuko awiri, Manase ndi Efuremu; ndipo sanawagawire Alevi kanthu m'dziko, koma mizinda yokhalamo ndi dziko lozungulirako likhale la zoweta zao ndi chuma chao.


Motero ana a Yosefe, Manase ndi Efuremu analandira cholowa chao,


Gawo la fuko la Manase ndi ili: pakuti anali woyamba wa Yosefe. Makiri mwana woyamba wa Manase, atate wa Giliyadi, popeza ndiye munthu wa nkhondo, anakhala nayo Giliyadi ndi Basani.


Ndipo panali pamene nthawi yake inafika, Hana anaima, nabala mwana wamwamuna; namutcha dzina lake Samuele, nati, Chifukwa ndinampempha kwa Yehova,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa