Ndipo mthenga wa Yehova anampeza iye pa kasupe wa madzi m'chipululu, pa kasupe wa panjira ya ku Suri.
Genesis 22:11 - Buku Lopatulika Koma mthenga wa Yehova anamuitana iye ndi mau odzera kumwamba, nati, Abrahamu, Abrahamu; ndi iye anati, Ndine pano. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma mthenga wa Yehova anamuitana iye ndi mau odzera kumwamba, nati, Abrahamu, Abrahamu; ndi iye anati, Ndine pano. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma mngelo wa Chauta adamuitana kuchokera kumwamba, adati, “Abrahamu, Abrahamu!” Iye adayankha kuti, “Ee, Ambuye!” Mngeloyo adati, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma mngelo wa Yehova anayitana Abrahamu kuchokera kumwamba nati, “Abrahamu! Abrahamu!” Iye anayankha kuti, “Ee Ambuye.” |
Ndipo mthenga wa Yehova anampeza iye pa kasupe wa madzi m'chipululu, pa kasupe wa panjira ya ku Suri.
Ndipo Mulungu anamva mau a mnyamatayo, ndi mthenga wa Mulungu anamuitana Hagara, ndi mau odzera kumwamba, nati kwa iye, Watani Hagara? Usaope; chifukwa Mulungu anamva mau a mnyamata kumene ali.
Tauka, nuukitse mnyamatayo, ndi kumgwira m'dzanja lako; chifukwa ndidzamuyesa iye mtundu waukulu.
Ndipo panali zitapita zimenezo, Mulungu anamuyesa Abrahamu nati kwa iye, Abrahamu; ndipo anati, Ndine pano.
Ndipo mthenga anati, Usaike dzanja lako pa mwana, usamchitire iye kanthu; chifukwa tsopano ndidziwa kuti iwe umuopa Mulungu wako, pakuti sunandikanize ine mwana wako, mwana wako wayekha.
nati, Pa Ine ndekha ndalumbira, ati Yehova, popeza wachita ichi, sunandikanize mwana wako, mwana wako yekha,
Yehova Mulungu wa Kumwamba, amene ananditenga ine kunyumba ya atate wanga, ku dziko la abale anga, amene ananena ndi ine, amene analumbirira ine kuti, Ndidzapatsa mbeu zako dziko ili; Iye adzatumiza mthenga wake akutsogolere, ndipo udzamtengere mwana wanga mkazi kumeneko.
Ndipo Israele anati kwa Yosefe, Kodi abale ako sadyetsa zoweta mu Sekemu? Tiyeni, ndikutuma iwe kwa iwo. Ndipo anati, Ndine pano.
mthenga amene anandiombola ine ku zoipa zonse, adalitse anyamatawa; dzina langa litchulidwe pa iwo, ndi dzina la makolo anga Abrahamu ndi Isaki; iwo akule, nakhale khamu pakati padziko lapansi.
Ndipo mthenga wa Yehova anamuonekera m'chilangali chamoto chotuluka m'kati mwa chitsamba; ndipo anapenya, ndipo taonani, chitsamba chilikuyaka moto, koma chosanyeka chitsambacho.
Pamene Yehova anaona kuti adapatuka kukapenya, Mulungu ali m'kati mwa chitsamba, anamuitana, nati, Mose, Mose. Ndipo anati, Ndili pano.
Ndipo ndinamva mau a Ambuye akuti, Ndidzatumiza yani, ndipo ndani adzatimukira ife? Ndipo ine ndinati, Ndine pano; munditumize ine.
Ndipo pamene tidagwa pansi tonse, ndinamva mau akunena kwa ine m'chinenedwe cha Chihebri, Saulo, Saulo, undilondalonderanji Ine? Nkukuvuta kutsalima pachotwikira.
Ndipo mthenga wa Yehova anakwera kuchokera ku Giligala kunka ku Bokimu. Ndipo anati, Ndinakukweretsani kuchokera ku Ejipito, ndi kulowetsa inu m'dziko limene ndinalumbirira makolo anu; ndipo ndinati, Sindidzathyola chipangano changa nanu ku nthawi yonse;
Ndipo Yehova anabwera, naimapo, namuitana monga momwemo, Samuele, Samuele. Pompo Samuele anayankha, Nenani, popeza mnyamata wanu akumva.