Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 26:14 - Buku Lopatulika

14 Ndipo pamene tidagwa pansi tonse, ndinamva mau akunena kwa ine m'chinenedwe cha Chihebri, Saulo, Saulo, undilondalonderanji Ine? Nkukuvuta kutsalima pachotwikira.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Ndipo pamene tidagwa pansi tonse, ndinamva mau akunena kwa ine m'chinenedwe cha Chihebri, Saulo, Saulo, undilondalonderanji Ine? Nkukuvuta kutsalima pachotwikira.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Tonse tidagwa pansi, ndipo ine ndidamva mau ondiwuza pa Chiyuda kuti, ‘Saulo, Saulo, ukundizunziranji? Ukungodzipweteka wekha ngati ng'ombe yoponda zidyali pa chobayira.’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Tonse tinagwa pansi ndipo ndinamva mawu mʼChihebri akuti, ‘Saulo, Saulo chifukwa chiyani ukundizunza Ine? Nʼkovuta kulimbikira mtunda wopanda madzi.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 26:14
11 Mawu Ofanana  

Nzeru yabwino ipatsa chisomo; koma njira ya achiwembu ili makolokoto.


Taonani, ndidzaika Yerusalemu akhale chipanda chodzandiritsa kwa mitundu yonse ya anthu yozungulirapo, ndipo chidzafikira Yuda yemwe pomangira misasa Yerusalemu.


Pakuti atero Yehova wa makamu: Utatha ulemererowo ananditumiza kwa amitundu amene anakufunkhani; pakuti iye wokhudza inu, akhudza mwana wa m'diso lake.


Ndipo m'mene adamlola, Paulo anaimirira pamakwerero, natambalitsira anthu dzanja; ndipo pokhala chete onse, analankhula nao m'chinenedwe cha Chihebri, nanena:


Ndipo pakumva kuti analankhula nao m'chinenedwe cha Chihebri, anaposa kukhala chete; ndipo anati,


dzuwa lamsana, ndinaona panjira, Mfumu, kuunika kochokera kumwamba kowalitsa koposa dzuwa kunawala pondizinga ine ndi iwo akundiperekeza.


Ndipo ndinati, Ndinu yani Mbuye? Ndipo Ambuye anati, Ine ndine Yesu amene iwe umlondalonda.


Ndipo amunawo akumperekeza iye anaima duu, atamvadi mau, koma osaona munthu.


Kapena kodi tichititsa nsanje Ambuye? Kodi mphamvu zathu ziposa Iye?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa