Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 31:11 - Buku Lopatulika

11 Mthenga wa Mulungu ndipo anati kwa ine m'kulotamo, Yakobo; nati ine, Ndine pano.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Mthenga wa Mulungu ndipo anati kwa ine m'kulotamo, Yakobo; nati ine, Ndine pano.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Ndipo mngelo wa Mulungu adalankhula nane m'maloto momwemo nandiitana kuti, ‘Yakobe,’ ine ndidayankha kuti, ‘Ee Ambuye!’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Kutulo komweko, mngelo wa Mulungu anati, ‘Yakobo.’ Ine ndinayankha, ‘Ee, Ambuye.’

Onani mutuwo Koperani




Genesis 31:11
21 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova anamuonekera iye pa mtengo yathundu ya ku Mamure, pamene anakhala pa khomo la hema wake pakutentha dzuwa.


Ndipo Yehova adati, Kodi ndidzabisira Abrahamu chimene ndichita?


Ndipo panali zitapita zimenezo, Mulungu anamuyesa Abrahamu nati kwa iye, Abrahamu; ndipo anati, Ndine pano.


Koma mthenga wa Yehova anamuitana iye ndi mau odzera kumwamba, nati, Abrahamu, Abrahamu; ndi iye anati, Ndine pano.


Ndipo mthenga wa Yehova anamuitana Abrahamu ndi mau odzera kumwamba kachiwiri,


Ndipo panali potenga mabere ziwetozo, ine ndinatukula maso anga, ndipo ndinapenya m'kulota, taonani, atonde okwera ziweto anali amipyololomipyololo, amathothomathotho, ndi amawangamawanga.


Ine ndine Mulungu wa ku Betele, kuja unathira mafuta pamwala paja, pamene unandilumbirira ine chilumbiriro: tsopano uka, nuchoke m'dziko lino, nubwerere ku dziko la abale ako.


Ndipo Mulungu anadza kwa Labani Mwaramu usiku, nati kwa iye, Tadziyang'anira wekha, usanene kwa Yakobo kapena zabwino kapena zoipa.


ndipo anati kwa iwo, Ndiona ine nkhope ya atate wanu kuti siindionekere ine monga kale; koma Mulungu wa atate wanga anali ndi ine.


Yosefe ndipo analota loto, nawafotokozera abale ake; ndipo anamuda iye koposa.


Ndipo Mulungu ananena kwa Israele, m'masomphenya a usiku, nati, Yakobo, Yakobo.


Pamene Yehova anaona kuti adapatuka kukapenya, Mulungu ali m'kati mwa chitsamba, anamuitana, nati, Mose, Mose. Ndipo anati, Ndili pano.


Pamenepo udzaitana, ndipo Yehova adzayankha; udzafuula ndipo Iye adzati, Ndine pano. Ngati uchotsa pakati pa iwe goli, kukodolana moipa, ndi kulankhula moipa,


Ndipo anati, Tamvani, tsono mau anga; pakakhala mneneri pakati pa inu, Ine Yehova ndidzizindikiritsa kwa iye m'masomphenya, ndinena naye m'kulota.


Ndipo pamene Pilato analikukhala pa mpando wakuweruza, mkazi wake anatumiza mau kwa iye, kunena, Musachite kanthu ndi munthu wolungamayo; pakuti lero m'kulota ine ndasauka kwambiri chifukwa cha Iye.


Pamenepo Eli anaitana Samuele, nati, Mwana wanga, Samuele. Nati iye, Ndine.


Pamenepo Yehova anaitana Samuele; ndipo iye anayankha kuti, Ndili pano.


Ndipo Yehova anabwereza kumuitana, ndi kuti, Samuele. Ndipo Samuele anauka, napita kwa Eli, nati, Ndine, pakuti mwandiitana ndithu. Koma iye anayankha, Sindinaitane, mwana wanga; kagone.


Ndipo Yehova anabwereza kumuitana Samuele nthawi yachitatu. Ndipo iye anauka napita kwa Eli, nati, Ndine, pakuti mwandiitana ndithu. Ndipo Eli anazindikira kuti ndiye Yehova amene analikuitana mwanayo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa