Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 31:10 - Buku Lopatulika

10 Ndipo panali potenga mabere ziwetozo, ine ndinatukula maso anga, ndipo ndinapenya m'kulota, taonani, atonde okwera ziweto anali amipyololomipyololo, amathothomathotho, ndi amawangamawanga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Ndipo panali potenga mabere ziwetozo, ine ndinatukula maso anga, ndipo ndinapenya m'kulota, taonani, atonde okwera ziweto anali amipyololomipyololo, amathothomathotho, ndi amawangamawanga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Pa nthaŵi yakuti zoŵeta zitenga maŵere, ine ndidalota maloto, ndipo ndidaona kuti atonde amene ankakwerawo anali amipyololomipyololo, amathothomathotho ndi amaŵangamaŵanga.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 “Pa nthawi imene ziweto zimatenga mawere ndinalota maloto, ndipo ndinaona kuti atonde onse amene ankakwerawo anali amichocholozi, amawangamawanga kapena amathothomathotho

Onani mutuwo Koperani




Genesis 31:10
11 Mawu Ofanana  

Ndipo Mulungu anati kwa iye m'kulota, Inde ndidziwa Ine, kuti wachita icho ndi mtima wangwiro, ndipo Inenso ndinakuletsa iwe kuti usandichimwire ine: chifukwa chake sindinakuloleze iwe kuti umkhudze mkaziyo.


Ndipo analota, taonani, makwerero anaima pansi, pamwamba pake ndipo padafikira kumwamba: ndipo, taonani, amithenga a Mulungu analinkukwera, analinkutsika pamenepo.


Ndipo ziweto zinatenga mabere patsogolo pa nthyolezo, ndipo zoweta zinabala zamipyololomipyololo, ndi mathothomathotho, ndi zamawangamawanga.


Mthenga wa Mulungu ndipo anati kwa ine m'kulotamo, Yakobo; nati ine, Ndine pano.


Ndipo anati, Tukulatu maso ako, nuone, atonde onse amene akwera zoweta ali amipyololomipyololo, amathothomathotho, ndi amawangamawanga: chifukwa ndaona zonse zimene Labani akuchitira iwe.


Ndipo Mulungu anadza kwa Labani Mwaramu usiku, nati kwa iye, Tadziyang'anira wekha, usanene kwa Yakobo kapena zabwino kapena zoipa.


Chomwecho Mulungu anazichotsa zoweta za atate wanu, nandipatsa ine.


Yosefe ndipo analota loto, nawafotokozera abale ake; ndipo anamuda iye koposa.


Ku Gibiyoni Yehova anaonekera Solomoni m'kulota usiku, nati Mulungu, Tapempha chimene ndikupatse.


Ndipo anati, Tamvani, tsono mau anga; pakakhala mneneri pakati pa inu, Ine Yehova ndidzizindikiritsa kwa iye m'masomphenya, ndinena naye m'kulota.


Akauka pakati pa inu mneneri, kapena wakulota maloto, nakakupatsani chizindikiro kapena chozizwa;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa