Ndipo anati, Tiyeni, timange mzinda ndi nsanja, pamutu pake pafikire kumwamba; ndipo tidzipangire ife tokha dzina kuti tisabalalike padziko lonse lapansi.
Genesis 11:3 - Buku Lopatulika Ndipo ananenana wina ndi wina, Tiyeni tipange njerwa, tiziotchetse. Ndipo anali ndi njerwa naziyesa miyala, ndi katondo anayesa matope. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ananenana wina ndi wina, Tiyeni tipange njerwa, tiziochetse. Ndipo anali ndi njerwa naziyesa miyala, ndi katondo anayesa matope. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono adayamba kuuzana kuti, “Tiyeni tiwumbe njerwa ndi kuzitentha.” Motero m'malo mwa miyala adatenga njerwa, namangira phula m'malo mwa matope. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono anawuzana kuti, “Tiyeni tiwumbe njerwa ndi kuziwotcha bwinobwino.” Tsono mʼmalo mwa miyala anagwiritsa ntchito njerwa zowotcha, ndipo mʼmalo mwa matope anagwiritsa ntchito phula. |
Ndipo anati, Tiyeni, timange mzinda ndi nsanja, pamutu pake pafikire kumwamba; ndipo tidzipangire ife tokha dzina kuti tisabalalike padziko lonse lapansi.
Tiyeni, titsike, pomwepo tisokoneze chinenedwe chao, kuti wina asamvere chinenedwe cha mnzake.
Chigwa cha Sidimu chinali ndi zitengetenge thoo; ndipo anathawa mafumu a ku Sodomu ndi Gomora nagwa m'menemo: amene anatsala anathawira kuphiri.
Natulutsa anthu a m'mzindamo, nawacheka ndi mipeni ya manomano, ndi nkhwangwa zachitsulo; nawapsitiriza ndi chitsulo, nawapititsa m'ng'anjo yanjerwa; natero ndi mizinda yonse ya ana a Amoni. Ndipo Davide ndi anthu onse anabwerera kunka ku Yerusalemu.
Alimbikitsana m'chinthu choipa; apangana za kutchera misampha mobisika; akuti, Adzaiona ndani?
nawawitsa moyo wao ndi ntchito yolimba, ya dothi ndi ya njerwa, ndi ntchito zonse za pabwalo, ntchito zao zonse zimene anawagwiritsa nzosautsa.
Koma pamene sanathe kum'bisanso, anamtengera kabokosi kagumbwa, napakapo nkhunga ndi phula; naikamo mwanayo, nakaika pakati pa mabango m'mbali mwa mtsinje.
Ndinati mumtima mwanga, Tiyetu, ndikuyese ndi chimwemwe; tapenya tsono zabwino; ndipo taona, ichinso ndi chabe.
Ndipo tsopano ndidzakuuzani chimene nditi ndichite ndi munda wanga wampesa; ndidzachotsapo tchinga lake, ndipo zidzadyedwa; ndidzagumula linga lake ndipo zidzapondedwa pansi;
anthu amene andiputa Ine kumaso kwanga nthawi zonse, apereka nsembe m'minda, nafukizira zonunkhira panjerwa;
Njerwa zagwa, koma ife tidzamanga ndi miyala yosema; mikuyu yagwetsedwa, koma tidzaisinthanitsa ndi mikungudza.
Udzitungiretu madzi a nthawi yokumangira misasa, limbikitsa malinga ako, lowa kuthope, ponda dothi, limbitsa ng'anjo yanjerwa.
ndipo tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino,
komatu dandaulirananani nokha tsiku ndi tsiku, pamene patchedwa, Lero; kuti angaumitsidwe wina wa inu ndi chenjerero la uchimo;
Nanga tsono, inu akunena, Lero kapena mawa tidzapita kulowa kumudzi wakutiwakuti, ndipo tidzagonerako ndi kutsatsa malonda, ndi kupindula nao;