Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Genesis 11:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Tsono anawuzana kuti, “Tiyeni tiwumbe njerwa ndi kuziwotcha bwinobwino.” Tsono mʼmalo mwa miyala anagwiritsa ntchito njerwa zowotcha, ndipo mʼmalo mwa matope anagwiritsa ntchito phula.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

3 Ndipo ananenana wina ndi wina, Tiyeni tipange njerwa, tiziotchetse. Ndipo anali ndi njerwa naziyesa miyala, ndi katondo anayesa matope.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndipo ananenana wina ndi wina, Tiyeni tipange njerwa, tiziochetse. Ndipo anali ndi njerwa naziyesa miyala, ndi katondo anayesa matope.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Tsono adayamba kuuzana kuti, “Tiyeni tiwumbe njerwa ndi kuzitentha.” Motero m'malo mwa miyala adatenga njerwa, namangira phula m'malo mwa matope.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 11:3
19 Mawu Ofanana  

Kenaka anati, “Tiyeni tidzimangire mzinda wokhala ndi nsanja yoti ikafike kumwamba kuti titchuke. Kupanda kutero tibalalikana pa dziko lonse lapansi.”


Tiyeni titsikireko tikasokoneze chiyankhulo chawo kuti asamamvetsetsane.”


Koma Chigwa cha Sidimu chinali chodzaza ndi maenje aphula. Choncho pamene mafumu a ku Sodomu ndi Gomora amathawa, ankhondo ena anagweramo ndipo ena anathawira ku mapiri.


ndipo anatulutsa anthu amene anali mʼmenemo, nawayika kuti azigwira ntchito ya macheka, yosula makasu ndi nkhwangwa, ndiponso yowomba njerwa. Davide anachita izi ndi mizinda yonse ya Aamoni. Kenaka iye pamodzi ndi gulu lake lonse lankhondo anabwerera ku Yerusalemu.


Iwo amalimbikitsana wina ndi mnzake pa chikonzero chawo choyipa, amayankhula zobisa misampha yawo; ndipo amati, “Adzayiona ndani?”


Aigupto anachititsa moyo wa Aisraeli kukhala owawa kwambiri powagwiritsa ntchito yakalavulagaga yowumba njerwa ndi kuponda dothi lomangira, pamodzi ndi ntchito zina zosiyanasiyana zamʼminda. Iwo anakakamiza Aisraeli mwankhanza kuti agwire ntchito yowawayi.


Koma mwanayo atafika pa msinkhu woti sakanathanso kubisidwa, amayi ake anatenga kadengu kopangidwa ndi bango nakamata phula. Kenaka anayika mwanayo mʼmenemo ndi kukamuyika pa mabango mu mtsinje wa Nailo.


Akadzati, “Tiye kuno; tikabisale kuti tiphe anthu, tikabisalire anthu osalakwa;


Ine ndinaganiza mu mtima mwanga, “Tsopano ndiyese zosangalatsa kuti ndipeze zomwe ndi zabwino.” Koma izi zinaonekanso kuti ndi zopandapake.


Tsopano ndikuwuzani chimene ndidzawuchitire munda wanga wa mpesa: ndidzachotsa mpanda wake, ndipo mundawo udzawonongeka; ndidzagwetsa khoma lake, ndipo nyama zidzapondapondamo.


Ndatambasulira manja anga anthu aja amene nthawi zonse amandikwiyitsa mopanda manyazi. Iwo amapereka nsembe mʼminda ndi kufukiza lubani pa maguwa ansembe a njerwa.


“Ngakhale njerwa zagumuka, koma ife tidzamanga ndi miyala yosema. Mitanda ya mkuyu yagwetsedwa, koma ife tidzayika mitanda ya mkungudza mʼmalo mwake.”


Tungani madzi woti mudzamwe nthawi ya kuzunguliridwa kwanu, limbitsani chitetezo chanu! Pondani dothi, ikani mʼchikombole, konzani khoma la njerwa!


Tiziganizira mmene tingalimbikitsirane wina ndi mnzake pokondana ndi kuchita ntchito zabwino.


Koma muzilimbikitsana tsiku ndi tsiku, ikanalipo nthawi imene imatchedwa kuti “Lero” kuti aliyense wa inu mtima wake usawumitsidwe ndi chinyengo cha tchimo.


Tsono tamverani, inu amene mumati, “Lero kapena mawa tipita ku mzinda wakutiwakuti, tikatha chaka chimodzi tikuchita malonda ndi kupanga ndalama.”


Tsono tamverani, inu anthu achuma, lirani ndi kufuwula chifukwa cha zovuta zimene zidzakugwereni.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa