2 Samueli 12:31 - Buku Lopatulika31 Natulutsa anthu a m'mzindamo, nawacheka ndi mipeni ya manomano, ndi nkhwangwa zachitsulo; nawapsitiriza ndi chitsulo, nawapititsa m'ng'anjo yanjerwa; natero ndi mizinda yonse ya ana a Amoni. Ndipo Davide ndi anthu onse anabwerera kunka ku Yerusalemu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201431 Natulutsa anthu a m'mudzimo, nawacheka ndi mipeni ya manomano, ndi nkhwangwa zachitsulo; nawapsitiriza ndi chitsulo, nawapititsa m'ng'anjo yanjerwa; natero ndi midzi yonse ya ana a Amoni. Ndipo Davide ndi anthu onse anabwerera kunka ku Yerusalemu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa31 Adaŵatulutsa anthu amumzindamo, nakaŵagwiritsa ntchito ndi masowo ndi mapiki ndi nkhwangwa, ndi kuŵaumbitsa njerwa. Umu ndimo m'mene adachitira ndi mizinda yonse ya Aamoni. Pambuyo pake Davide adabwerera ku Yerusalemu pamodzi ndi ankhondo onse. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero31 ndipo anatulutsa anthu amene anali mʼmenemo, nawayika kuti azigwira ntchito ya macheka, yosula makasu ndi nkhwangwa, ndiponso yowomba njerwa. Davide anachita izi ndi mizinda yonse ya Aamoni. Kenaka iye pamodzi ndi gulu lake lonse lankhondo anabwerera ku Yerusalemu. Onani mutuwo |