Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 1:14 - Buku Lopatulika

14 nawawitsa moyo wao ndi ntchito yolimba, ya dothi ndi ya njerwa, ndi ntchito zonse za pabwalo, ntchito zao zonse zimene anawagwiritsa nzosautsa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 nawawitsa moyo wao ndi ntchito yolimba, ya dothi ndi ya njerwa, ndi ntchito zonse za pabwalo, ntchito zao zonse zimene anawagwiritsa nzosautsa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Moyo wa Aisraele unali woŵaŵa chifukwa cha ntchito yakalavulagaga youmba njerwa, ndiponso ntchito zosiyanasiyana zam'minda. Ankaŵakakamiza mwankhanza kugwira ntchito zonse zolemetsa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Aigupto anachititsa moyo wa Aisraeli kukhala owawa kwambiri powagwiritsa ntchito yakalavulagaga yowumba njerwa ndi kuponda dothi lomangira, pamodzi ndi ntchito zina zosiyanasiyana zamʼminda. Iwo anakakamiza Aisraeli mwankhanza kuti agwire ntchito yowawayi.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 1:14
30 Mawu Ofanana  

Ndipo anati kwa Abramu, Dziwitsa ndithu kuti mbeu zako zidzakhala alendo m'dziko la eni, ndipo zidzatumikira iwo, ndipo iwo adzasautsa izo zaka mazana anai;


nalankhula nao monga mwa uphungu wa achinyamata, nati, Atate wanga analemeretsa goli lanu, koma ine ndidzaonjezerapo pa goli lanu; atate wanga anakukwapulani ndi zikoti, koma ine ndidzakukwapulani ndi zinkhanira.


Anandisautsa kawirikawiri kuyambira ubwana wanga, anene tsono Israele;


Pogona inu m'makola a zoweta, mukhala ngati mapiko a njiwa okulira ndi siliva, ndi nthenga zake zokulira ndi golide woyenga wonyezimira.


Ndinamchotsera katundu paphewa pake, manja ake anamasuka ku chotengera.


Potero anawaikira akulu a misonkho kuti awasautse ndi akatundu ao. Ndipo anammangira Farao mizinda yosungiramo chuma, ndiyo Pitomu ndi Ramsesi.


Ndipo Aejipito anawagwiritsa ana a Israele ntchito yosautsa;


Ndipo mfumu ya Aejipito inanena ndi anamwino a Ahebri, dzina lake la wina ndiye Sifira, dzina la mnzake ndiye Puwa;


Ndipo kunali pakupita masiku ambiri aja, idafa mfumu ya Aejipito; ndi ana a Israele anatsitsa moyo chifukwa cha ukapolo wao, nalira, ndi kulira kwao kunakwera kwa Mulungu chifukwa cha ukapolowo.


Ine ndine Yehova Mulungu wako, amene ndinatulutsa iwe ku dziko la Ejipito, kunyumba ya ukapolo.


Ndipo Mose ananena chomwecho ndi ana a Israele; koma sanamvere Mose chifukwa cha kuwawa mtima, ndi ukapolo wolemera.


Monga mkango wobangula ndi chilombo choyendayenda, momwemo mfumu yoipa ya anthu osauka.


Chifukwa chake atero Ambuye, Yehova wa makamu, Inu anthu anga okhala mu Ziyoni, musaope Asiriya; ngakhale amenya inu ndi chibonga, kapena kukusamulira iwe ndodo yake, monga amachitira Ejipito.


Wokantha anthu mwaukali kuwakantha chikanthire, wolamulira amitundu mokwiya, angosautsidwa wopanda womlanditsa.


Ndidzachiika m'dzanja la iwo amene avutitsa iwe; amene anena kumoyo wako, Gwada pansi kuti ife tipite; ndipo iwe wagonetsa pamsana pako monga pansi, ndi monga khwalala kwa iwo amene apita pamenepo.


Chifukwa chake kodi ndichitenji pano? Ati Yehova; popeza anthu anga achotsedwa popanda kanthu? Akuwalamulira awaliritsa, ati Yehova; ndipo dzina langa lichitidwa mwano tsiku lonse kosalekeza.


Kodi kumeneku si kusala kudya kumene ndinakusankha: kumasula nsinga za zoipa, ndi kumasula zomanga goli, ndi kuleka otsenderezedwa amuke mfulu, ndi kuti muthyole magoli onse?


Usamamweruza momzunza; koma uope Mulungu wako.


Ndipo muwayese cholowa cha ana anu akudza m'mbuyo, akhale aoao; muwayese akapolo kosatha; koma za abale anu, ana a Israele, musamalamulirana mozunza.


Akhale naye monga wolipidwa chaka ndi chaka; asamamlamulira momzunza pamaso pako.


inu amene mukudyanso mnofu wa anthu anga; ndi kusenda khungu lao ndi kuthyola mafupa ao; inde awaduladula ngati nyama yoti aphike, ndi ngati nyama ya mumphika.


Udzitungiretu madzi a nthawi yokumangira misasa, limbikitsa malinga ako, lowa kuthope, ponda dothi, limbitsa ng'anjo yanjerwa.


kuti makolo athu anatsikira kunka ku Ejipito, ndipo tinakhala mu Ejipito masiku ambiri; ndipo Aejipito anachitira zoipa ife, ndi makolo athu.


Imeneyo inachenjerera fuko lathu, niwachitira choipa makolo athu, niwatayitsa tiana tao, kuti tingakhale ndi moyo.


Kuona ndaona choipidwa nacho anthu anga ali mu Ejipito, ndipo amva kubuula kwao; ndipo ndatsika kuwalanditsa; ndipo tsopano, tiye kuno, ndikutume ku Ejipito.


koma Aejipito anatichitira choipa, natizunza, natisenza ntchito yolimba.


Koma Yehova anakutengani, nakutulutsani m'ng'anjo yamoto, mu Ejipito, mukhale kwa Iye anthu a cholowa chake, monga mukhala lero lino.


Koma ananena nao, Musanditcha Naomi, munditche Mara; pakuti Wamphamvuyonse anandichitira zowawa ndithu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa