Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 14:10 - Buku Lopatulika

10 Chigwa cha Sidimu chinali ndi zitengetenge thoo; ndipo anathawa mafumu a ku Sodomu ndi Gomora nagwa m'menemo: amene anatsala anathawira kuphiri.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Chigwa cha Sidimu chinali ndi zitengetenge thoo; ndipo anathawa mafumu a ku Sodomu ndi Gomora nagwa m'menemo: amene anatsala anathawira kuphiri.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Chigwa cha Sidimu chinali chodzaza ndi maenje a phula. Tsono anthu a ku Sodomu ndi Gomora adagonja nathaŵa nkhondo, ndipo adagwa m'maenjemo, koma ena adathaŵira ku mapiri.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Koma Chigwa cha Sidimu chinali chodzaza ndi maenje aphula. Choncho pamene mafumu a ku Sodomu ndi Gomora amathawa, ankhondo ena anagweramo ndipo ena anathawira ku mapiri.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 14:10
12 Mawu Ofanana  

Ndipo ananenana wina ndi wina, Tiyeni tipange njerwa, tiziotchetse. Ndipo anali ndi njerwa naziyesa miyala, ndi katondo anayesa matope.


Ndipo anatenga chuma chonse cha Sodomu ndi Gomora ndi zakudya zao zonse, namuka.


Ndipo anatuluka mfumu ya Sodomu kukomana naye, atabwera anatha kuwakantha Kedorilaomere ndi mafumu amene anali naye, ku chigwa cha Save (ndiko ku chigwa cha mfumu),


Mfumu ya Sodomu ndipo inati kwa Abramu, Ndipatse ine anthu, nutenge chuma iwe wekha.


Onse amenewo anadziphatikana pa chigwa cha Sidimu (pamenepo ndi pa Nyanja ya Mchere).


ndi Kedorilaomere mfumu ya Elamu, ndi Tidala mfumu ya Goimu, ndi Amurafere mfumu ya Sinara, ndi Ariyoki mfumu ya Elasara; mafumu anai kumenyana ndi asanu.


Ndipo panali pamene anawatulutsa iwo kunja, anati, Tapulumuka ndi moyo wako; usacheuke, usakhale pachigwa paliponse; thawira kuphiri, kuti unganyeke.


Ndipo Loti anabwera kutuluka mu Zowari nakhala m'phiri ndi ana aakazi awiri pamodzi naye: chifukwa anaopa kukhala mu Zowari, ndipo anakhala m'phanga, iye ndi ana ake aakazi.


amene anaonongeka ku Endori; anakhala ngati ndowe ya kumunda.


Ndipo padzali, kuti iye amene athawa mbiri yoopsa, adzagwa m'dzenje; ndi iye amene atuluka m'kati mwa dzenje, adzakodwa mumsampha, pakuti mazenera a kuthambo atsegudwa, ndi maziko a dziko agwedezeka.


Ndipo iye wakuthawa chifukwa cha mantha adzagwa m'dzenje; ndi iye amene atuluka m'dzenje adzagwidwa m'khwekhwe; pakuti ndidzatengera pa iye, pa Mowabu, chaka cha kulangidwa kwao, ati Yehova.


Ndipo kunali, atatha Israele kupha nzika zonse za ku Ai, kuthengo, kuchipululu kumene anawapirikitsira, natha onse kugwa ndi lupanga lakuthwa mpaka adathedwa onse, Aisraele onse anabwerera ku Ai, naukantha ndi lupanga lakuthwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa