Zikhale zounikira m'thambo la kumwamba, kuti ziunikire padziko lapansi; ndipo kunatero.
Genesis 1:16 - Buku Lopatulika Ndipo Mulungu anapanga zounikira zazikulu ziwiri; chounikira chachikulu chakulamulira usana, chounikira chaching'ono chakulamulira usiku, ndi nyenyezi zomwe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Mulungu anapanga zounikira zazikulu ziwiri; chounikira chachikulu chakulamulira usana, chounikira chaching'ono chakulamulira usiku, ndi nyenyezi zomwe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Motero Mulungu adalenga miyuni iŵiri yaikulu: dzuŵa loŵala masana, ndi mwezi woŵala usiku. Adalenganso nyenyezi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mulungu anapanga zowunikira zazikulu ziwiri; chachikulu chilamulire usana ndi chachingʼono chilamulire usiku. Iye anapanganso nyenyezi. |
Zikhale zounikira m'thambo la kumwamba, kuti ziunikire padziko lapansi; ndipo kunatero.
muja nyenyezi za m'mawa zinaimba limodzi mokondwera, ndi ana onse a Mulungu anafuula ndi chimwemwe?
Kutuluka kwake lituluka kolekezera thambo, ndipo kuzungulira kwake lifikira ku malekezero ake; ndipo kulibe kanthu kobisalira kutentha kwake.
Pakuona ine thambo la kumwamba lanu, ntchito ya zala zanu, mwezi ndi nyenyezi, zimene munazikhazika,
Chifukwa nyenyezi za kumwamba ndi makamu ao sizidzawala; dzuwa lidzada m'kutuluka kwake, ndipo mwezi sudzaonetsa kuwala kwake.
Pompo mwezi udzanyazitsidwa, ndi dzuwa lidzakhala ndi manyazi, pakuti Yehova wa makamu adzalamulira chaulemerero m'phiri la Ziyoni, ndi mu Yerusalemu, ndi pamaso pa akuluakulu ake.
Kwezani maso anu kumwamba, muone amene analenga izo, amene atulutsa khamu lao ndi kuziwerenga; azitcha zonse maina ao, ndi mphamvu zake zazikulu, ndi popeza ali wolimba mphamvu, palibe imodzi isoweka.
Ine ndilenga kuyera ndi mdima, Ine ndilenga mtendere ndi choipa, Ine ndine Yehova wochita zinthu zonse zimenezi.
Yehova atero, amene apatsa dzuwa kuti liunikire usana, ndi malemba a mwezi ndi a nyenyezi kuti aunikire usiku, amene atonthoza nyanja, pamene mafunde ake agavira; Yehova wa makamu ndi dzina lake:
Dzuwa ndi mwezi zinaima njera mokhala mwao; pa kuunika kwa mivi yanu popita iyo. Pa kung'anipa kwa nthungo yanu yonyezimira.
Koma pomwepo, atapita masauko a masiku awo, dzuwa lidzadetsedwa, ndi mwezi sudzaonetsa kuwala kwake, ndi nyenyezi zidzagwa kuchokera kumwamba, ndi mphamvu za kumwamba zidzagwedezeka:
Ndipo ora lachisanu ndi chimodzi panali mdima padziko lonse, kufikira ora lachisanu ndi chinai.
Kuli ulemerero wa dzuwa, ndi ulemerero wina wa mwezi, ndi ulemerero wina wa nyenyezi; pakuti nyenyezi isiyana ndi nyenyezi mu ulemerero.
ndi kuti mungakweze maso anu kupenya kumwamba, ndipo poona dzuwa ndi mwezi ndi nyenyezi, khamu lonse la kumwamba, munganyengedwe ndi kuzigwadira, ndi kuzitumikira, zimene Yehova Mulungu wanu anagawira mitundu yonse ya anthu pansi pa thambo lonse.
Ndipo pamzinda sipafunika dzuwa, kapena mwezi wakuuwalira; pakuti ulemerero wa Mulungu uunikira umenewu, ndipo nyali yake ndiye Mwanawankhosa.