1 Akorinto 15:41 - Buku Lopatulika41 Kuli ulemerero wa dzuwa, ndi ulemerero wina wa mwezi, ndi ulemerero wina wa nyenyezi; pakuti nyenyezi isiyana ndi nyenyezi mu ulemerero. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201441 Kuli ulemerero wa dzuwa, ndi ulemerero wina wa mwezi, ndi ulemerero wina wa nyenyezi; pakuti nyenyezi isiyana ndi nyenyezi m'ulemerero. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa41 Dzuŵa lili ndi kuŵala kwake, mwezi uli ndi kuŵala kwake kosiyana ndi kwa dzuŵa kuja, nyenyezinso zili ndi kuŵala kwake kosiyana ndi kwa zina zija. Ngakhale nyenyezizo zimasiyananso kuŵala kwake. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero41 Dzuwa lili ndi ulemerero wake, ndipo pali ulemerero wina wa mwezi, palinso ulemerero winanso wa nyenyezi. Ulemerero wa nyenyezi ndi wosiyanasiyana. Onani mutuwo |