Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Genesis 1:16 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Mulungu anapanga zowunikira zazikulu ziwiri; chachikulu chilamulire usana ndi chachingʼono chilamulire usiku. Iye anapanganso nyenyezi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

16 Ndipo Mulungu anapanga zounikira zazikulu ziwiri; chounikira chachikulu chakulamulira usana, chounikira chaching'ono chakulamulira usiku, ndi nyenyezi zomwe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Ndipo Mulungu anapanga zounikira zazikulu ziwiri; chounikira chachikulu chakulamulira usana, chounikira chaching'ono chakulamulira usiku, ndi nyenyezi zomwe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Motero Mulungu adalenga miyuni iŵiri yaikulu: dzuŵa loŵala masana, ndi mwezi woŵala usiku. Adalenganso nyenyezi.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 1:16
22 Mawu Ofanana  

zikhale kuthambo kuti ziwunikire pa dziko lapansi. Ndipo zinachitikadi.”


ngati pamene ndinaona dzuwa likuwala, kapena mwezi ukuyenda mwa ulemerero wake,


pamene nyenyezi za kummawa zinkayimba pamodzi ndipo angelo onse a Mulungu ankafuwula mokondwa?


Mutamandeni, inu dzuwa ndi mwezi, mutamandeni, inu nonse nyenyezi zowala.


Zonse zitamande dzina la Yehova pakuti Iye analamula ndipo zinalengedwa.


Limatuluka kuyambira mbali ina ya thambo ndi kuzungulira mpaka mbali inanso; palibe chinthu chotha kupewa kutentha kwake.


Masana ndi anu ndipo usiku ndi wanunso; Inuyo munakhazikitsa dzuwa ndi mwezi.


Pamene ndilingalira za mayiko anu akumwamba, ntchito ya zala zanu, mwezi ndi nyenyezi, zimene mwaziyika pa malo ake,


Nyenyezi zakumwamba ndiponso zonse zamlengalenga sizidzaonetsa kuwala kwawo. Dzuwa lidzada potuluka, ndipo mwezi sudzawala konse.


Mwezi udzanyazitsidwa, dzuwa lidzachita manyazi; pakuti Yehova Wamphamvuzonse adzakhala mfumu ndipo adzalamulira; pa Phiri la Ziyoni ndi ku Yerusalemu, ndipo adzaonetsa ulemerero wake pamaso pa akuluakulu.


Tayangʼanani mlengalenga ndipo onani. Kodi ndani analenga zonsezi mukuzionazi? Yehova ndiye amene amazitsogolera ngati gulu la ankhondo, nayitana iliyonse ndi dzina lake. Ndipo popeza Iye ali ndi nyonga zambiri, palibe ndi imodzi yomwe imene inasowapo.


Ndimalenga kuwala ndi mdima, ndimabweretsa madalitso ndi tsoka; ndine Yehova, amene ndimachita zonsezi.


Yehova akuti, Iye amene amakhazikitsa dzuwa kuti liziwala masana, amene amalamula kuti mwezi ndi nyenyezi ziziwala usiku, amene amavundula nyanja kuti mafunde akokome, dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse:


Dzuwa ndi mwezi zinayima chilili mlengalenga, pa kungʼanima kwa mivi yanu yowulukayo, pa kunyezimira kwa mkondo wanu.


“Akadzangotha mavuto a masiku amenewo, “ ‘dzuwa lidzadetsedwa, ndipo mwezi sudzawala; nyenyezi zidzagwa kuchokera kumwamba, ndipo mphamvu za mmwamba zidzagwedezeka.’


Kuyambira 12 koloko masana mpaka 3 koloko, kunachita mdima pa dziko lonse.


Dzuwa lili ndi ulemerero wake, ndipo pali ulemerero wina wa mwezi, palinso ulemerero winanso wa nyenyezi. Ulemerero wa nyenyezi ndi wosiyanasiyana.


Ndipo pamene muyangʼana kumwamba muona dzuwa, mwezi ndi nyenyezi, zonse zakumwambazo musakopeke kuti muzigwadire ndi kumapembedza zinthu zimene Yehova wapereka kwa anthu a mitundu yonse pa dziko lapansi.


Palibe chifukwa choti dzuwa kapena mwezi ziwale popeza mu mzindawo ulemerero wa Mulungu ndiwo umawalamo ndipo nyale yake ndi Mwana Wankhosa uja.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa