Ndipo Yehova anavumbitsa pa Sodomu ndi pa Gomora miyala ya sulufure ndi moto kutuluka kwa Mulungu kumwamba;
Eksodo 9:23 - Buku Lopatulika Pamenepo Mose anasamulira ndodo yake kuthambo, ndipo Yehova anatumiza bingu ndi matalala, ndi moto unatsikira pansi; ndipo Yehova anavumbitsa matalala padziko la Ejipito. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo Mose anasamulira ndodo yake kuthambo, ndipo Yehova anatumiza bingu ndi matalala, ndi moto unatsikira pansi; ndipo Yehova anavumbitsa matalala pa dziko la Ejipito. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mose adakweza ndodo yake kumwamba. Pompo Chauta adatumiza mabingu ndi matalala, ndipo mphezi zidaomba pa nthaka. Chauta adagwetsa matalala pa dziko la Ejipito. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mose ataloza ndodo yake kumwamba, Yehova anatumiza mabingu ndi matalala ndi ziphaliwali zongʼanima pa nthaka. Kotero Yehova anagwetsa matalala pa dziko la Igupto. |
Ndipo Yehova anavumbitsa pa Sodomu ndi pa Gomora miyala ya sulufure ndi moto kutuluka kwa Mulungu kumwamba;
Ndipo anagunda m'mwamba Yehova, ndipo Wam'mwambamwamba anamvetsa liu lake; matalala ndi makala amoto.
Liu la bingu lanu linatengezanatengezana; mphezi zinaunikira ponse pali anthu; dziko lapansi linanjenjemera ndi kugwedezeka.
Ndipo kunali tsiku lachitatu, m'mawa, panali mabingu ndi zimphezi, ndi mtambo wakuda bii paphiripo, ndi liu la lipenga lolimbatu; ndi anthu onse okhala kutsasa ananjenjemera.
Ndipo anthu onse anaona mabingu ndi zimphezi, ndi liu la lipenga ndi phiri lilikufuka; ndipo pamene anthu anaziona, ananjenjemera, naima patali.
Taona, mawa monga nthawi ino ndidzavumbitsa mvumbi wa matalala, sipadakhale unzake mu Ejipito kuyambira tsiku lija lidakhazikika kufikira lero lino.
Potero panali matalala, ndi moto wakutsikatsika pakati pa matalala, choopsa ndithu; panalibe chotere m'dziko lonse la Ejipito chiyambire mtundu wao.
Ndipo Yehova adzamveketsa mau ake a ulemerero, ndipo adzaonetsa kumenya kwa dzanja lake, ndi mkwiyo wake waukali, ndi lawi la moto wonyambita, ndi kuomba kwa mphepo, ndi mkuntho ndi matalala.
Ndipo ndidzalimbana naye ndi mliri ndi mwazi; ndipo ndidzamvumbitsira iye, ndi magulu ake, ndi mitundu yambiri ya anthu okhala naye mvumbi waukulu, ndi matalala aakulu, moto ndi sulufure.
Ndipo kunali, pakuthawa iwo pamaso pa Israele, potsikira pa Betehoroni, Yehova anawagwetsera miyala yaikulu yochokera kumwamba mpaka pa Azeka, nafa iwo; akufa ndi miyala yamatalala anachuluka ndi iwo amene ana a Israele anawapha ndi lupanga.
ndipo panakhala mphezi, ndi mau, ndi mabingu; ndipo panali chivomezi chachikulu chotero sichinaoneke chiyambire anthu padziko, chivomezi cholimba chotero, chachikulu chotero.
Ndipo anatsika kumwamba matalala aakulu, lonse lolemera ngati talente, nagwa pa anthu; ndipo anthu anachitira Mulungu mwano chifukwa cha mliri wa matalala, pakuti mliri wake ndi waukulu ndithu.
Ndipo woyamba anaomba lipenga, ndipo panakhala matalala ndi moto, zosakaniza ndi mwazi, ndipo anazitaya padziko lapansi; ndipo limodzi la magawo atatu a dziko lidapserera, ndipo limodzi la magawo atatu a mitengo lidapserera, ndipo msipu wonse udapserera.