Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 19:16 - Buku Lopatulika

16 Ndipo kunali tsiku lachitatu, m'mawa, panali mabingu ndi zimphezi, ndi mtambo wakuda bii paphiripo, ndi liu la lipenga lolimbatu; ndi anthu onse okhala kutsasa ananjenjemera.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Ndipo kunali tsiku lachitatu, m'mawa, panali mabingu ndi zimphezi, ndi mtambo wakuda bii paphiripo, ndi liu la lipenga lolimbatu; ndi anthu onse okhala kutsasa ananjenjemera.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Tsono m'maŵa, pa tsiku lakelo, panali mabingu ndi mphezi paphiripo. Kunalinso mtambo wochindikira, ndiponso kulira kwakukulu kwa mbetete. Anthu onse m'mahemamo ankangonjenjemera ndi mantha.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Mʼmamawa wa tsiku lachitatu kunali mabingu, ziphaliwali ndi mtambo wakuda umene unaphimba phiri, ndiponso lipenga lolira kwambiri. Aliyense ku misasa kuja ananjenjemera ndi mantha.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 19:16
31 Mawu Ofanana  

Anaweramitsa miyambanso, natsika; ndipo mdima wandiweyani unali pansi pa mapazi ake.


ndipo ansembe sanakhoze kuimirira kutumikira chifukwa cha mtambowo; pakuti ulemerero wa Yehova unadzaza nyumba ya Mulungu.


Ndani anachikumbira mchera chimvula, kapena njira ya bingu la mphezi,


Adzafika Mulungu wathu, ndipo sadzakhala chete. Moto udzanyeka pankhope pake, ndipo pozungulira pake padzasokosera kwakukulu.


Liu la bingu lanu linatengezanatengezana; mphezi zinaunikira ponse pali anthu; dziko lapansi linanjenjemera ndi kugwedezeka.


Tamvani, anthu anga, ndidzakuchitirani mboni; Israele, ukadzandimvera!


Mphezi zake zinaunikira dziko lokhalamo anthu; dziko lapansi linaona nilinagwedezeka.


Nakonzekeretu tsiku lachitatu; pakuti tsiku lachitatu Yehova adzatsika paphiri la Sinai pamaso pa anthu onse.


Ndipo anati kwa anthu, Mukonzekeretu tsiku lachitatu nimusayandikiza mkazi.


Ndipo Mose anatulutsa anthu kutsasa, kuti akomane ndi Mulungu; ndipo anaima patsinde paphiri.


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Taona, ndikudza kwa iwe mu mtambo wakuda bii, kuti anthu amve pamene ndilankhula ndi iwe, ndi kuti akuvomereze nthawi zonse. Pakuti Mose adauza Yehova mau a anthuwo.


Ndipo anthu onse anaona mabingu ndi zimphezi, ndi liu la lipenga ndi phiri lilikufuka; ndipo pamene anthu anaziona, ananjenjemera, naima patali.


Ndipo anthu anaima patali, koma Mose anayandikiza ku mdima waukulu kuli Mulungu.


Pamenepo mtambo unaphimba chihema chokomanako, ndi ulemerero wa Yehova unadzaza Kachisiyo.


Pamenepo Mose anasamulira ndodo yake kuthambo, ndipo Yehova anatumiza bingu ndi matalala, ndi moto unatsikira pansi; ndipo Yehova anavumbitsa matalala padziko la Ejipito.


Kodi simundiopa Ine? Ati Yehova: simudzanthunthumira pamaso pa Ine, amene ndinaika mchenga chilekaniro cha nyanja, ndi lemba lamuyaya kuti isapitirirepo? Ndipo ngakhale mafunde ake achita gavigavi, alephera; ngakhale akokoma, sangathe kupitirirapo.


Yehova ndiye wolekerera mkwiyo, koma wa mphamvu yaikulu; ndi wosamasula ndithu wopalamula; njira ya Yehova ili m'kamvulumvulu ndi mumkuntho; ndipo mitambo ndiyo fumbi la mapazi ake.


Ndipo Iye adzatumiza angelo ake ndi kulira kwakukulu kwa lipenga, ndipo iwo adzasonkhanitsa osankhidwa ake kumphepo zinai, kuyambira malekezero a thambo kufikira malekezero ake ena.


(ndinalinkuima pakati pa Yehova ndi inu muja, kukulalikirani mau a Yehova; popeza munachita mantha chifukwa cha moto, osakwera m'phirimo) ndi kuti:


ndipo maonekedwewo anali oopsa otere, kuti Mose anati, Ndiopatu ndi kunthunthumira.


Ndinagwidwa ndi Mzimu tsiku la Ambuye, ndipo ndinamva kumbuyo kwanga mau aakulu, ngati a lipenga,


Ndipo anatsegulidwa Kachisi wa Mulungu amene ali mu Mwamba; ndipo linaoneka likasa la chipangano chake, mu Kachisi mwake, ndipo panali mphezi, ndi mau, ndi mabingu, ndi chivomezi, ndi matalala aakulu.


Zitatha izi ndinapenya, ndipo taonani, khomo lotseguka mu Mwamba, ndipo mau oyamba ndinawamva, ngati lipenga lakulankhula ndi ine, anati, Kwera kuno, ndipo ndidzakuonetsa zimene ziyenera kuchitika m'tsogolomo.


Ndipo mu mpando wachifumu mudatuluka mphezi ndi mau ndi mabingu. Ndipo panali nyali zisanu ndi ziwiri za moto zoyaka kumpando wachifumu, ndiyo mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu;


Ndipo mngeloyo anatenga mbale ya zofukiza, naidzaza ndi moto wopala paguwa la nsembe, nauponya padziko lapansi; ndipo panakhala mabingu, ndi mau, ndi mphezi, ndi chivomezi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa