Eksodo 19:16 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero16 Mʼmamawa wa tsiku lachitatu kunali mabingu, ziphaliwali ndi mtambo wakuda umene unaphimba phiri, ndiponso lipenga lolira kwambiri. Aliyense ku misasa kuja ananjenjemera ndi mantha. Onani mutuwoBuku Lopatulika16 Ndipo kunali tsiku lachitatu, m'mawa, panali mabingu ndi zimphezi, ndi mtambo wakuda bii paphiripo, ndi liu la lipenga lolimbatu; ndi anthu onse okhala kutsasa ananjenjemera. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201416 Ndipo kunali tsiku lachitatu, m'mawa, panali mabingu ndi zimphezi, ndi mtambo wakuda bii paphiripo, ndi liu la lipenga lolimbatu; ndi anthu onse okhala kutsasa ananjenjemera. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa16 Tsono m'maŵa, pa tsiku lakelo, panali mabingu ndi mphezi paphiripo. Kunalinso mtambo wochindikira, ndiponso kulira kwakukulu kwa mbetete. Anthu onse m'mahemamo ankangonjenjemera ndi mantha. Onani mutuwo |
Kodi simuyenera kuchita nane mantha?” Akutero Yehova. “Kodi simuyenera kunjenjemera pamaso panga? Ine ndinayika mchenga kuti ukhale malire a nyanja, malire a muyaya amene nyanjayo singadutsepo. Mafunde angawombe motani, koma sangathe kupitirira malirewo; mafunde angakokome motani, koma sangadutse malirewo.