Eksodo 9:23 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero23 Mose ataloza ndodo yake kumwamba, Yehova anatumiza mabingu ndi matalala ndi ziphaliwali zongʼanima pa nthaka. Kotero Yehova anagwetsa matalala pa dziko la Igupto. Onani mutuwoBuku Lopatulika23 Pamenepo Mose anasamulira ndodo yake kuthambo, ndipo Yehova anatumiza bingu ndi matalala, ndi moto unatsikira pansi; ndipo Yehova anavumbitsa matalala padziko la Ejipito. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201423 Pamenepo Mose anasamulira ndodo yake kuthambo, ndipo Yehova anatumiza bingu ndi matalala, ndi moto unatsikira pansi; ndipo Yehova anavumbitsa matalala pa dziko la Ejipito. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa23 Mose adakweza ndodo yake kumwamba. Pompo Chauta adatumiza mabingu ndi matalala, ndipo mphezi zidaomba pa nthaka. Chauta adagwetsa matalala pa dziko la Ejipito. Onani mutuwo |