Chivumbulutso 8:7 - Buku Lopatulika7 Ndipo woyamba anaomba lipenga, ndipo panakhala matalala ndi moto, zosakaniza ndi mwazi, ndipo anazitaya padziko lapansi; ndipo limodzi la magawo atatu a dziko lidapserera, ndipo limodzi la magawo atatu a mitengo lidapserera, ndipo msipu wonse udapserera. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20147 Ndipo woyamba anaomba lipenga, ndipo panakhala matalala ndi moto, zosanganiza ndi mwazi, ndipo anazitaya pa dziko lapansi; ndipo limodzi la magawo atatu a dziko lidapserera, ndipo limodzi la magawo atatu a mitengo lidapserera, ndipo msipu wonse udapserera. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa7 Mngelo woyamba adaliza lipenga lake. Atatero, padadza matalala ndi moto zosanganizika ndi magazi. Zimenezi zidaponyedwa pa dziko lapansi, ndipo chimodzi mwa zigawo zitatu za dziko ndi za mitengo chidapsa. Pamenepo padapsanso udzu wonse wauŵisi. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero7 Mngelo woyamba anayimba lipenga lake ndipo kunabwera matalala ndi moto wosakanizana ndi magazi ndipo unaponyedwa pa dziko lapansi. Gawo limodzi la magawo atatu a dziko lapansi linapsa, gawo limodzi la magawo atatu a mitengo linapsa ndi gawo limodzi la magawo atatu a udzu wauwisi linapsanso. Onani mutuwo |