Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 9:18 - Buku Lopatulika

18 Taona, mawa monga nthawi ino ndidzavumbitsa mvumbi wa matalala, sipadakhale unzake mu Ejipito kuyambira tsiku lija lidakhazikika kufikira lero lino.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Taona, mawa monga nthawi yino ndidzavumbitsa mvumbi wa matalala, sipadakhala unzake m'Ejipito kuyambira tsiku lija lidakhazikika kufikira lero lino.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Imvani tsono, nthaŵi yomwe ino maŵa, ndidzagwetsa matalala amphamvu amene sanagwepo nkale lonse mu Ejipito muno chiyambire cha dziko lino.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Nʼchifukwa chake mawa, nthawi ngati ino, ndidzagwetsa matalala amphamvu amene sanagwepo pa Igupto, kuyambira pachiyambi mpaka lero.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 9:18
14 Mawu Ofanana  

Tsono Yezebele anatuma mthenga kwa Eliya, wakuti, Milungu indilange nionjezepo, ngati sindilinganiza moyo wako ndi moyo wa mmodzi wa iwowo mawa nthawi yomwe ino.


koma mawa dzuwa lino ndidzatuma anyamata anga kwa iwe, nadzafunafuna m'nyumba mwako, ndi m'nyumba za anyamata ako; ndipo kudzakhala kuti chifuniro chonse cha maso ako adzachigwira ndi manja ao, nadzachichotsa.


Ndipo Elisa anati, Mverani mau a Yehova; atero Yehova, Mawa dzuwa lino adzagula muyeso wa ufa ndi sekeli, adzagulanso miyeso iwiri ya barele ndi sekeli, pa chipata cha Samariya.


Ndipo kunachitika, monga adanena munthu wa Mulungu kwa mfumu, ndi kuti, Adzagula miyeso iwiri ya barele ndi sekeli, adzagulanso muyeso wa ufa ndi sekeli; kudzatero mawa, dzuwa lino, pa chipata cha Samariya;


ngati aufikitsira dziko lake kulidzudzula, kapena kulichitira chifundo.


Kodi unalowa m'zosungiramo chipale chofewa? Kapena unapenya zosungiramo matalala,


amene ndiwasungira tsiku la nsautso, tsiku lakulimbana nkhondo?


Momwemo muwatsate ndi namondwe, nimuwaopse ndi kamvulumvulu wanu.


Ndipo dzombe linakwera padziko lonse la Ejipito, ndipo linatera pakati pa malire onse Ejipito, lambirimbiri; lisanafike ili panalibe dzombe lotere longa ili, ndipo litapita ili sipadzakhalanso lotere.


ndipo lidzadzaza m'nyumba zako, ndi m'nyumba za anyamata ako onse, ndi m'nyumba za Aejipito onse; sanachione chotere atate ako kapena makolo ako, kuyambira tsiku lija lakukhala iwo padziko lapansi kufikira lero lino. Ndipo anatembenuka, natuluka kwa Farao.


Ndipo kudzakhala kulira kwakukulu m'dziko lonse la Ejipito, kunalibe kunzake kotere, sikudzakhalanso kunzake kotere.


Kodi udzikwezanso pa anthu anga, ndi kusawalola amuke?


Ndipo anatsika kumwamba matalala aakulu, lonse lolemera ngati talente, nagwa pa anthu; ndipo anthu anachitira Mulungu mwano chifukwa cha mliri wa matalala, pakuti mliri wake ndi waukulu ndithu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa