Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 18:13 - Buku Lopatulika

13 Ndipo anagunda m'mwamba Yehova, ndipo Wam'mwambamwamba anamvetsa liu lake; matalala ndi makala amoto.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Ndipo anagunda m'mwamba Yehova, ndipo Wam'mwambamwamba anamvetsa liu lake; matalala ndi makala amoto.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Kumwamba Chauta adagunda ngati bingu, Wopambanazonse liwu lake lidamveka m'kati mwa matalala ndi makala amoto.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Yehova anabangula kumwamba ngati bingu, mawu a Wammwambamwamba anamveka ponseponse.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 18:13
18 Mawu Ofanana  

Kodi uli nalo dzanja ngati Ine Mulungu? Kapena ukhoza kugunda ndi mau ngati Ine?


Pa kudzudzula kwanu anathawa; anathawa msanga liu la bingu lanu;


Adzagwetsa pwatapwata misampha pa oipa; moto ndi miyala ya sulufure, ndi mphepo yoopsa zidzawagawikira m'chikho chao.


Makala amoto awagwere; aponyedwe kumoto; m'maenje ozama, kuti asaukenso.


Naperekanso zoweta zao kwa matalala, ndi ng'ombe zao kwa mphezi.


Ndipo anthu onse anaona mabingu ndi zimphezi, ndi liu la lipenga ndi phiri lilikufuka; ndipo pamene anthu anaziona, ananjenjemera, naima patali.


Potero panali matalala, ndi moto wakutsikatsika pakati pa matalala, choopsa ndithu; panalibe chotere m'dziko lonse la Ejipito chiyambire mtundu wao.


Ndipo mkokomo wa mapiko a akerubi unamveka mpaka bwalo lakunja, ngati mau a Mulungu Wamphamvuyonse, pakunena Iye.


Patsogolo pake panapita mliri, ndi makala amoto anatuluka pa mapazi ake.


Chifukwa chake khamu la anthu akuimirirako, ndi kuwamva ananena kuti kwagunda. Ena ananena, Mngelo walankhula ndi Iye.


Adzaonda nayo njala adzanyekeka ndi makala a moto, chionongeko chowawa; ndipo ndidzawatumizira mano a zilombo, ndi ululu wa zokwawa m'fumbi.


Ndipo kunali, pakuthawa iwo pamaso pa Israele, potsikira pa Betehoroni, Yehova anawagwetsera miyala yaikulu yochokera kumwamba mpaka pa Azeka, nafa iwo; akufa ndi miyala yamatalala anachuluka ndi iwo amene ana a Israele anawapha ndi lupanga.


Ndipo ndinamva ngati mau a khamu lalikulu, ngati mkokomo wa madzi ambiri, ngati mau a mabingu olimba, ndi kunena, Aleluya; pakuti achita ufumu Ambuye Mulungu wathu, Wamphamvuyonse.


Ndipo mu mpando wachifumu mudatuluka mphezi ndi mau ndi mabingu. Ndipo panali nyali zisanu ndi ziwiri za moto zoyaka kumpando wachifumu, ndiyo mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu;


Ndipo mngeloyo anatenga mbale ya zofukiza, naidzaza ndi moto wopala paguwa la nsembe, nauponya padziko lapansi; ndipo panakhala mabingu, ndi mau, ndi mphezi, ndi chivomezi.


Ndipo pamene Samuele analikupereka nsembe yopserezayo, Afilisti anayandikira kuti aponyane ndi Aisraele; koma tsiku lomwe lija Yehova anagunda ndi kugunda kwakukulu pa Afilistiwo, nawapolonganitsa. Ndipo anakanthidwa pamaso pa Aisraele.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa