Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 18:14 - Buku Lopatulika

14 Ndipo anatuma mivi yake nawabalalitsa; inde mphezi zaunyinji, nawamwaza.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Ndipo anatuma mivi yake nawabalalitsa; inde mphezi zaunyinji, nawamwaza.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Adaponya mivi yake nabalalitsa adani ake, adachititsa zing'aning'ani, naŵapirikitsa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Iye anaponya mivi yake nabalalitsa adani ake, ndi zingʼaningʼani zake anawagonjetsa.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 18:14
20 Mawu Ofanana  

Mau abuma kuitsata, agunda ndi mau a ukulu wake, ndipo sailetsa atamveka mau ake.


Mulungu agunda modabwitsa ndi mau ake, achita zazikulu osazidziwa ife.


Kodi ukhoza kutumiza mphezi kuti zimuke, ndi kunena nawe, Tili pano?


Pakuti mivi ya Wamphamvuyonse yandilowa, mzimu wanga uwumwa ulembe wake; zoopsa za Mulungu zindindandira nkhondo.


Ng'animitsani mphezi, ndi kuwabalalitsa; tumizani mivi yanu, ndi kuwapirikitsa.


Pakuti mudzawabweza m'mbuyo, popiringidza m'nsinga zanu pankhope pao.


Liu la Yehova lili pamadzi; Mulungu wa ulemerero agunda, ndiye Yehova pamadzi ambiri.


Liu la Yehova ligawa malawi a moto.


Makongwa anatsanula madzi; thambo lidamvetsa liu lake; mivi yanu yomwe inatulukira.


Liu la bingu lanu linatengezanatengezana; mphezi zinaunikira ponse pali anthu; dziko lapansi linanjenjemera ndi kugwedezeka.


Ndipo Yehova adzamveketsa mau ake a ulemerero, ndipo adzaonetsa kumenya kwa dzanja lake, ndi mkwiyo wake waukali, ndi lawi la moto wonyambita, ndi kuomba kwa mphepo, ndi mkuntho ndi matalala.


ndipo Yehova amveketsa mau ake pamaso pa khamu lake la nkhondo; pakuti a m'chigono mwake ndi ambirimbiri; pakuti Iye wakuchita mau ake ndiye wamphamvu ndithu; pakuti tsiku la Yehova ndi lalikulu ndi loopsa ndithu; akhoza kupirira nalo ndani?


Dzuwa ndi mwezi zinaima njera mokhala mwao; pa kuunika kwa mivi yanu popita iyo. Pa kung'anipa kwa nthungo yanu yonyezimira.


Mulungu amtulutsa mu Ejipito; ali nayo mphamvu yonga ya njati; adzawadya amitundu, ndiwo adani ake. Nadzamphwanya mafupa ao, ndi kuwapyoza ndi mivi yake.


Ndidzawaunjikira zoipa; ndidzawathera mivi yanga.


Mivi yanga ndiiledzeretsa nao mwazi, ndi lupanga langa lidzalusira nyama; ndi mwazi wa ophedwa ndi ogwidwa, ndi mutu wachitsitsi wa mdani.


Ndipo Yehova anawamwaza pamaso pa Israele, ndipo anawakantha makanthidwe aakulu ku Gibiyoni, nawapirikitsa panjira yokwera pa Betehoroni, nawakantha mpaka Azeka, ndi mpaka Makeda.


Otsutsana ndi Yehova adzaphwanyika; kumwamba Iye adzagunda pa iwo; Yehova adzaweruza malekezero a dziko. Ndipo adzapatsa mphamvu mfumu yake, nadzakweza nyanga ya wodzozedwa wake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa