Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 18:15 - Buku Lopatulika

15 Ndipo zidaoneka zoyendamo madzi, nafukuka maziko a dziko lapansi, mwa kudzudzula kwanu, Yehova, mwa mpumo wa mpweya wa m'mphuno mwanu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Ndipo zidaoneka zoyendamo madzi, nafukuka maziko a dziko lapansi, mwa kudzudzula kwanu, Yehova, mwa mpumo wa mpweya wa m'mphuno mwanu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Ngalande zozama zam'nyanja zidaonekera, maziko a dziko lapansi adakhala poyera, pamene Inu Chauta mudakhuluma mokalipa, pamene mudatulutsa mpweya wamphamvu m'mphuno mwanu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Zigwa za mʼnyanja zinaonekera poyera; maziko a dziko lapansi anakhala poyera, Yehova atabangula mwaukali, pamene mpweya wamphamvu unatuluka mʼmphuno mwanu.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 18:15
22 Mawu Ofanana  

Pamenepo m'munsi mwa nyanja munaoneka, maziko a dziko anaonekera poyera, ndi mtonzo wa Yehova, ndi mpumo wa mpweya wa m'mphuno mwake.


Taonani, ndidzalonga mwa iye mzimu wakuti adzamva mbiri, nadzabwerera kunka ku dziko lake, ndipo ndidzamgwetsa ndi lupanga m'dziko lake.


Akutidwa manja ake ndi mphezi, nailamulira igwere pofunapo Iye.


Atayika ndi mpweya wa Mulungu, nathedwa ndi mpumo wa mkwiyo wake.


anakhazika dziko lapansi pa maziko ake, silidzagwedezeka kunthawi yonse.


Ndipo anadzudzula Nyanja Yofiira, ndipo inaphwa: Potero anawayendetsa mozama ngati m'chipululu.


Ng'animitsani mphezi, ndi kuwabalalitsa; tumizani mivi yanu, ndi kuwapirikitsa.


Mudagawa kasupe ndi mtsinje; mudaphwetsa mitsinje yaikulu.


Pa kudzudzula kwanu, Mulungu wa Yakobo, galeta ndi kavalo yemwe anagwa m'tulo.


Liu la bingu lanu linatengezanatengezana; mphezi zinaunikira ponse pali anthu; dziko lapansi linanjenjemera ndi kugwedezeka.


Koma munakweza nyanga yanga ngati ya njati; anandidzoza mafuta atsopano.


Ndipo ndi mpumo wa m'mphuno mwanu madzi anaunjikika, mayendedwe ake anakhala chilili ngati mulu; zozama zinalimba m'kati mwa nyanja.


koma ndi chilungamo adzaweruza aumphawi, nadzadzudzulira ofatsa a m'dziko moongoka; ndipo adzamenya dziko lapansi ndi chibonga cha kukamwa kwake, nadzapha oipa ndi mpweya wa milomo yake.


Pakuti Tofeti wakonzedwa kale, inde chifukwa cha mfumu wakonzedweratu; Iye wazamitsapo, nakuzapo; mulu wakewo ndi moto ndi nkhuni zambiri; mpweya wa Yehova uuyatsa ngati mtsinje wa sulufure.


Atero Yehova, Ngati ukhoza kuyesa thambo la kumwamba, ndi kusanthula pansi maziko a dziko, pamenepo ndidzachotsa mbeu zonse za Israele chifukwa cha zonse anazichita, ati Yehova.


Ndinatsikira kumatsinde a mapiri, mipingiridzo ya dziko inanditsekereza kosatha; koma munandikwezera moyo wanga kuuchotsa kuchionongeko, Yehova Mulungu wanga.


Tamverani, mapiri inu, chitsutsano cha Yehova, ndi inu maziko olimba a dziko lapansi; pakuti Yehova ali nacho chitsutsano ndi anthu ake, ndipo adzatsutsana ndi Israele.


Ndipo Yehova adzaoneka pamwamba pao, ndi muvi wake udzatuluka ngati mphezi; ndipo Ambuye Mulungu adzaomba lipenga, nadzayenda ndi akamvulumvulu a kumwera.


Ndipo pamene Samuele analikupereka nsembe yopserezayo, Afilisti anayandikira kuti aponyane ndi Aisraele; koma tsiku lomwe lija Yehova anagunda ndi kugunda kwakukulu pa Afilistiwo, nawapolonganitsa. Ndipo anakanthidwa pamaso pa Aisraele.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa